Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:1 - Buku Lopatulika

1 Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Munthu akaba ng'ombe kapena nkhosa, nkuipha kapena kuigulitsa, alipire ng'ombe zisanu pa ng'ombe imodzi, kapena nkhosa zinai pa nkhosa imodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:1
9 Mawu Ofanana  

ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.


Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.


Popanda zoweta modyera muti see; koma mphamvu ya ng'ombe ichulukitsa phindu.


koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.


Ndiponso m'nsalu zako wapezeka mwazi wa miyoyo ya aumphawi osachimwa; sunawapeze pakuboola, koma ponsepo.


woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.


azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo.


Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa