Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 21:36 - Buku Lopatulika

36 Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

36 Kapena kudadziwika kuti ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, koma osaisunga mwiniyo, azilipa ndithu, ng'ombe kulipa ng'ombe, koma yakufayo ndi yake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

36 Koma kukadziŵika kuti ng'ombeyo inkangogunda anthu, mwiniwake osaimanga, mwiniwakeyo ayenera kulipira pakupereka ng'ombe yamoyo chifukwa cha yakufayo. Tsono ng'ombe yakufayo ikhale yake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

36 Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 21:36
4 Mawu Ofanana  

Koma ngati ng'ombe ikatunga masiku adapitawo, ndipo anamchenjeza mwiniyo, koma osaisunga iye, ndipo ikapha mwamuna kapena mkazi, aiponye miyala ng'ombeyo, ndi mwini wakeyo amuphenso.


Ng'ombe ya mwini ikapweteka ng'ombe ya mnzake, nifa, azigulitsa ng'ombe yamoyoyo, nagawe ndalama zake; naigawe, ndi yakufa yomweyo.


Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.


Munthu akakantha nyama kuti ife, ambwezere ina; moyo kulipa moyo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa