Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Miyambo 11:3 - Buku Lopatulika

3 Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Kuongoka mtima kwa olungama kuwatsogolera; koma kukhota kwa achiwembu kudzawaononga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Ungwiro wa anthu olungama umaŵatsogolera, koma makhalidwe okhota a anthu onyenga ngoononga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera, koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

Onani mutuwo Koperani




Miyambo 11:3
13 Mawu Ofanana  

Ungwiro ndi kuongoka mtima zindisunge, pakuti ndayembekezera Inu.


Mundiweruze, Yehova, pakuti ndayenda mu ungwiro wanga, ndipo ndakhulupirira Yehova, sindadzaterereka.


Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake; koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.


Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira; koma udyo ugwetsa wochimwa.


Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake; mtima wake udandaula pa Yehova.


Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo.


Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola; chifukwa akana kuchita chiweruzo.


Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa; koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.


Woyenda mwangwiro adzapulumuka; koma wokhota m'mayendedwe ake adzagwa posachedwa.


Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?


Koma kupasula kwa olakwa ndi kwa ochimwa kudzakhala kumodzi, ndi iwo amene asiya Yehova adzathedwa.


Ndipo anapha mafumu a Amidiyani pamodzi ndi ophedwa ao ena; ndiwo Evi, ndi Rekemu, ndi Zuri, ndi Huri, ndi Reba, mafumu asanu a Amidiyani; namupha Balamu mwana wa Beori ndi lupanga.


Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa