Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zefaniya 3:13 - Buku Lopatulika

13 Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Otsala a Israele sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m'kamwa mwao simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwaopsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Otsala a mu Israeleŵa sadzalakwanso, sadzalankhulanso zabodza, sadzachitanso zonyenga, Adzakhala pabwino mwamtendere, popanda wina woŵaopsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Aisraeli otsala sadzachitanso zolakwika; sadzayankhulanso zonama, ngakhale chinyengo sichidzatuluka mʼkamwa mwawo. Adzadya ndi kugona ndipo palibe amene adzawachititse mantha.”

Onani mutuwo Koperani




Zefaniya 3:13
46 Mawu Ofanana  

Nuchita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wake anampumulitsira pozungulirapo.


Inde udzagona pansi, wopanda wina wakukunjenjemeretsa, ndipo ambiri adzakupembedza.


inde, sachita chosalungama; ayenda m'njira zake.


Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.


Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe?


Andigonetsa kubusa lamsipu, anditsogolera kumadzi odikha.


Mizinda ya Aroere yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsa.


Ndipo kudzakhala khwalala kumeneko, ndi njira, ndipo idzatchedwa njira yopatulika; odetsedwa sadzapita m'menemo; koma Iye adzakhala nao oyenda m'njira, ngakhale opusa, sadzasochera m'menemo.


M'chilungamo iwe udzakhazikitsidwa, udzakhala kutali ndi chipsinjo, pakuti sudzaopa; udzakhala kutali ndi mantha, pakuti sadzafika chifupi ndi iwe.


Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi m'menemo, lidzadyedwanso; monga kachere, ndi monganso thundu, imene tsinde lake likhalabe ataigwetsa; chotero mbeu yopatulika ndiyo tsinde lake.


Anthu ako adzakhalanso onse olungama; dzikolo lidzakhala cholowa chao kunthawi zonse, nthambi yooka Ine, ntchito ya manja anga, kuti Ine ndikuzidwe.


Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangachite monyenga; chomwecho Iye anali Mpulumutsi wao.


Ndipo Saroni adzakhala podyetsera nkhosa, ndi chigwa cha Akori chidzakhala pogona zoweta kwa anthu anga amene andifuna Ine.


Ndipo ndidzaziikira abusa amene adzazidyetsa; sadzaopanso, kapena kutenga nkhawa, sipadzasowa mmodzi yense, ati Yehova.


Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israele; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutali, ndi mbeu zako kudziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala chete, palibe amene adzamuopsa.


Koma ili ndi pangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israele atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzaika chilamulo changa m'kati mwao, ndipo m'mtima mwao ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, nadzakhala iwo anthu anga;


Ndipo adzasenza manyazi ao, ndi zolakwa zao zonse, zimene anandilakwira nazo, pokhala mosatekeseka iwo m'dziko lao, opanda wina wakuwaopsa;


Momwemo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu wakukhala mu Ziyoni, phiri langa lopatulika; pamenepo Yerusalemu adzakhala wopatulika, osapitanso alendo pakati pake,


Ndipo ndidzayeretsa mwazi wao umene sindinauyeretsa, pakuti Yehova akhala mu Ziyoni.


Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.


Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.


ndipo wotsimphinayo ndidzamuyesa wotsala, ndi iye wotayidwa kutali mtundu wamphamvu; ndipo Yehova adzakhala mfumu yao m'phiri la Ziyoni kuyambira pamenepo kufikira kosatha.


Mudyetse anthu anu ndi ndodo yanu, nkhosa za cholowa chanu zokhala pazokha m'nkhalango pakati pa Karimele, zidye mu Basani ndi mu Giliyadi masiku a kale lomwe.


Ndipo dziko la kunyanja lidzakhala la otsala a nyumba ya Yuda; adzadyetsa zoweta zao pamenepo; madzulo adzagona m'nyumba za Asikeloni; pakuti Yehova Mulungu wao adzawazonda, nadzabweza undende wao.


Yehova pakati pake ali wolungama; sadzachita chosalungama, m'mawa ndi m'mawa aonetsera chiweruzo chake poyera, chosasowa kanthu; koma wosalungama sadziwa manyazi.


Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.


Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;


Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.


Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika,


Yesu anaona Natanaele alinkudza kwa Iye, nanena za iye, Onani, Mwisraele ndithu, mwa iye mulibe chinyengo!


musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,


Komatu ngatinso mukumva zowawa chifukwa cha chilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;


Tidziwa kuti yense wobadwa kuchokera mwa Mulungu sachimwa, koma iye wobadwa kuchokera mwa Mulungu adzisunga yekha, ndipo woipayo samkhudza.


Ndipo m'kamwa mwao simunapezedwe bodza; ali opanda chilema.


ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa