Zefaniya 3:14 - Buku Lopatulika14 Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israele; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Imbani mokweza, inu anthu a ku Ziyoni! Fuulani inu Aisraele! Sangalalani, kondwani ndi mtima wonse, inu okhala mu Yerusalemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Imba, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni; fuwula mokweza, iwe Israeli! Sangalala ndi kukondwera ndi mtima wako wonse, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu! Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.