Ndikufuna tikambirane za zinthu zimene Mulungu amaziona ngati zonyansa. M'buku lakale la chipangano, nthawi zambiri Mulungu ankalankhula za mafano ndi miyambo ya anthu osamudziwa Iye, monga kupembedza milungu yabodza. Izi zinali zonyansa kwa Iye. Mulungu ankauza anthu ake kuti asiye zimenezi, chifukwa sizinali zimene amawafunira.
Mwachitsanzo, m'buku la Deuteronomio 18:9-121, Mulungu amatitchula zamatsenga ndi ufiti ngati zinthu zomunyansa pamaso pake. Ngakhale m'chipangano chatsopano, Yesu anatiphunzitsa kufunika kwa moyo woyera. M'buku la Mateyu 15:18-202, Iye ananena kuti zinthu zotuluka m'kamwa mwathu, monga mabodza ndi mawu otukwana, zimatichititsa kukhala onyansa, chifukwa zimachokera mumtima. Mulungu amaona kuipa kulikonse mumtima mwathu ngati konyansa.
Mulungu amafuna kuti tikhale oyera ndi omvera mawu ake. Tiziyesetsa kupewa zinthu zimene Iye amaziona ngati zonyansa. Kuphunzira Baibulo n'kofunika kwambiri kuti tidziwe zimene Mulungu amafuna ndikupewa kuchita zinthu zomunyansa pamaso pake. Tikatero, tidzakhala paubwenzi wabwino ndi Iye.
Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.
Musamabwera nayo mphotho ya wachigololo, kapena mtengo wake wa galu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha chowinda chilichonse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.
Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao.
Mafano osema a milungu yao muwatenthe ndi moto; musamasirira siliva ndi golide zili pa iwo, kapena kudzitengera izi; mungakodwe nazo; pakuti izi zinyansira Yehova Mulungu wanu. Musamalowa nacho chonyansachi m'nyumba mwanu, kuti mungaonongeke konse pamodzi nacho; muziipidwa nacho konse, ndi kunyansidwa nacho konse; popeza ndi chinthu choyenera kuonongeka konse.
Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.
ndipo simudzalowa konse momwemo kanthu kalikonse kosapatulidwa kapena iye wakuchita chonyansa ndi bodza; koma iwo okha olembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa.
Musamaphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya ng'ombe, kapena nkhosa, yokhala nacho chilema, kapena chilichonse choipa; pakuti chinyansira Yehova Mulungu wanu.
Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo chifukwa cha zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu.
Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.
Mkazi asavale chovala cha mwamuna, kapena mwamuna asavale chovala cha mkazi; pakuti aliyense wakuchita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.
Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo.
Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.
Koma muzichita nao motero: mukapasule maguwa ao a nsembe, ndi kuphwanya zoimiritsa zao, ndi kulikha zifanizo zao, ndi kutentha mafano ao osema ndi moto.
Pakuti onse akuchita zinthu izi, onse akuchita chisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m'thambo la kumwamba, kapena za m'dziko lapansi, kapena za m'madzi a pansi padziko. Usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje, wakulanga ana chifukwa cha atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai wa iwo amene akudana ndi Ine;
panalinso anyamata ochitirana dama m'dzikomo; iwo amachita monga mwa zonyansitsa za amitundu, amene Yehova anapirikitsa pamaso pa ana a Israele.
Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
Koma zilizonse zilibe zipsepse ndi mamba m'nyanja, ndi m'mitsinje, mwa zonse zokwawa za m'madzi, ndi mwa zamoyo zonse zili m'madzi, muziziyesa zonyansa; inde muziyese zonyansa; musamadya nyama zao; mitembo yao zikunyansireni. Zilizonse zopanda zipsepse kapena mamba m'madzimo muziyese zonyansa. Ndipo mwa mbalame muziziyesa zonyansa izi; simuyenera kuzidya, zonyansa ndi izi: mphungu, ndi nkhwazi, ndi chikambi;
Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, ntchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse ayankhe ndi kuti, Amen.
Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;
Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.
Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.
Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi mu Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Ndipo anadzikuza, nachita chonyansa pamaso panga; chifukwa chake ndinawachotsa pakuchiona.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, uona kodi izi alikuzichita? Zonyansa zazikulu nyumba ya Israele ilikuzichita kuno, kuti ndichoke kutali kwa malo anga opatulika? Koma udzaonanso zonyansa zina zoposa.
ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi?
Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota. Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu. Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.
Ndipo mkazi anavala chibakuwa, ndi mlangali, nakometsedwa ndi golide, ndi miyala ya mtengo wake, ndi ngale; nakhala nacho m'dzanja lake chikho chagolide chodzala ndi zonyansitsa, ndi zodetsa za chigololo chake, ndipo pamphumi pake padalembedwa dzina, CHINSINSI, BABILONI WAUKULU, AMAI WA ACHIGOLOLO NDI WA ZONYANSITSA ZA DZIKO.
Usamaipsa mwana wako wamkazi ndi kumchititsa chigololo; lingadzale ndi chigololo dzikoli, ndi kudzazidwa nazo zochititsa manyazi.
Taonani, inu muli achabe, ndi ntchito yanu yachabe; wonyansa ali iye amene asankha inu.
Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu. (Pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa) lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu. Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao. Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao. Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako.
M'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakuchepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzachita chifundo.
Koma ndinatuma kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndinauka mamawa ndi kuwatuma, ndi kuti, Musachitetu chonyansa ichi ndidana nacho.
Ndipo mfumu inawaipitsira misanje yokhala kum'mawa kwa Yerusalemu, ndiyo ya ku dzanja lamanja la phiri la chionongeko, imene Solomoni mfumu ya Israele adaimangira Asitaroti chonyansa cha Asidoni, ndi Kemosi chonyansa cha Mowabu, ndi Milikomu chonyansa cha ana a Amoni.
Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.
Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.
Palibe wina wokumbukira, kapena kudziwa, kapena kuzindikira, ndi kuti, Ndatentha mbali ina pamoto, inde ndaotchanso mkate pamakala pake, ndakazinga nyama ndi kuidya; kodi ndichipange chotsala chake, chikhale chonyansa? Ndidzagwadira kodi tsinde la mtengo?
Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.
Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lao pathupi pao, ndi mnofu wao pa mafupa ao;
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita chonyansa? Iai, sanakhale konse ndi manyazi, sanathe kunyala; chifukwa chake adzagwa mwa iwo akugwa; panthawi pamene ndidzafika kwa iwo, adzagwetsedwa, ati Yehova.
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.
Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda.
Kunja kuli agalu ndi anyanga, ndi achigololo, ndi ambanda, ndi opembedza mafano, ndi yense wakukonda bodza ndi kulichita.
Koma sendererani kuno chifupi, inu ana aamuna a watsenga, mbeu yachigololo ndi yadama. Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?
Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.
Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.
Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?
Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.
M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.
Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.
Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino.
Chodabwitsa ndi choopsa chaoneka m'dzikomo; aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?
Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, chifukwa cha zonyansa zao zonse anazichita.
Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.
Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.
Ndipo Yehova sanathe kupirirabe, chifukwa cha machitidwe anu oipa, ndi chifukwa cha zonyansa zimene munazichita; chifukwa chake dziko lanu likhala bwinja, ndi chizizwitso, ndi chitemberero, lopanda wokhalamo, monga lero lomwe.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwini, popeza wachita chigololo ndi mkazi wa mnansi wake, awaphe ndithu, mwamuna ndi mkazi onse awiri. Munthu akagona naye mkazi wa atate wake, wavula atate wake; awaphe ndithu onse awiri; mwazi wao ukhale pamutu pao. Munthu akagona ndi mpongozi wake, awaphe onse awiri; achita chisokonezo; mwazi wao ukhale pamutu pao. Munthu akagonana ndi mwamuna mnzake, monga amagonana ndi mkazi, achita chonyansa onse awiri; awaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao. Munthu akatenga mkazi pamodzi ndi mai wake chochititsa manyazi ichi; aziwatentha ndi moto, iye ndi iwowa; kuti pasakhale chochititsa manyazicho pakati pa inu. Mwamuna akagona ndi nyama amuphe ndithu; muiphenso nyamayi. Mkazi akasendera kwa nyama iliyonse kugonana nayo, umuphe mkaziyo, ndi nyama yomwe; muwaphe ndithu; mwazi wao ukhale pamutu pao. Munthu akatenga mlongo wake, mwana wamkazi wa atate wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, nakaona thupi lake, ndi mlongoyo akaona thupi lake; chochititsa manyazi ichi; ndipo awasadze pamaso pa ana a anthu ao; anavula mlongo wake; asenze mphulupulu yake. Munthu akagona ndi mkazi ali mumsambo, nakamvula, anavula kasupe wake, ndi iye mwini anavula kasupe wa nthenda yake; awadule onse awiri pakati pa anthu a mtundu wao. Usamavula mbale wa mai wako, kapena mlongo wa atate wako; popeza anavula abale ake; asenze mphulupulu yao. Unenenso kwa ana a Israele ndi kuti, Aliyense wa ana a Israele, kapena wa alendo akukhala mu Israele, amene apereka mbeu zake kwa Moleki, azimupha ndithu; anthu a m'dziko amponye miyala. Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa atate wake, navula mbale wa atate wake; asenze kuchimwa kwao; adzafa osaona ana. Munthu akatenga mkazi wa mbale wake, chodetsa ichi; wavula mbale wake; adzakhala osaona ana. Potero muzisunga malemba anga onse, ndi maweruzo anga onse, kuwachita; lingakusanzeni inu dziko limene ndipita nanuko, kuti mukhale m'mwemo. Musamatsata miyambo ya mtundu umene ndiuchotsa pamaso panu; popeza anachita izi zonse, ndinalema nao. Koma ndanena nanu, Mudzalandira dziko lao inu, ndipo Ine ndilipereka kwa inu likhale lanu, ndilo dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakusiyanitsani ndi mitundu ina ya anthu. Potero musiyanitse pakati pa nyama zoyera ndi nyama zodetsa, ndi pakati pa mbalame zodetsa ndi zoyera; ndipo musadzinyansitsa ndi nyama, kapena mbalame, kapena ndi kanthu kalikonse kakukwawa pansi, kamene ndinakusiyanitsirani kakhale kodetsa. Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga. Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu; aziwaponya miyala; mwazi wao ukhale pamutu pao. Ndipo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi kumsadza kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake; popeza anapereka a mbeu zake kwa Moleki, kudetsa nako malo anga opatulika, ndi kuipsa dzina langa lopatulika. Ndipo ngati anthu a m'dzikomo akambisa munthuyo pang'ono ponse, pamene apereka a mbeu zake kwa Moleki, kuti asamuphe; pamenepo nkhope yanga idzatsutsana naye munthuyo, ndi banja lake, ndi kumsadza iye, ndi onse akumtsata ndi chigololo kukachita chigololo kwa Moleki, kuwachotsa pakati pa anthu a mtundu wao.
Chifukwa andisiya Ine, nayesa malo ano achilendo, nafukizira m'menemo milungu ina, imene sanaidziwe, iwowa, ndi makolo ao ndi mafumu a Yuda; nadzaza malo ano ndi mwazi wa osachimwa; namanga misanje ya Baala, kuti apsereze ana ao m'menemo nsembe zopsereza za Baala, chimene sindinawauze, sindinachinene, sichinalowe m'mtima mwanga;
Ndipo anati kwa ine, Wachiona ichi, wobadwa ndi munthu iwe? Chinthu chopepuka ichi kodi ndi nyumba ya Yuda, kuti achite zonyansa azichita kunozi? Pakuti anadzaza dziko ndi chiwawa, nabwereranso kuutsa mkwiyo wanga, ndipo taonani, aika nthambi kumphuno kwao.
Ndidana nao, ndinyoza zikondwerero zanu, sindidzakondwera nayo misonkhano yanu yoletsa. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine. Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu. Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi; amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen. Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao.
Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele.
ndi nyumba za Yerusalemu, ndi nyumba za mafumu a Yuda, zimene ziipitsidwa, zidzanga malo a Tofeti, ndizo nyumba zonse anafukizira khamu lonse la kumwamba pa matsindwi ao, ndi kuithirira milungu ina nsembe zothira.
Koma nditi kuti zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziwanda osati kwa Mulungu; ndipo sindifuna kuti inu muyanjane ndi ziwanda. Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.
dzichenjerani nokha mungakodwe ndi kuwatsata, ataonongeka pamaso panu; ndi kuti mungafunsire milungu yao, ndi kuti, Amitundu awa atumikira milungu yao bwanji? Ndichite momwemo inenso.
Pakuti kupanduka kuli ngati choipa cha kuchita nyanga, ndi mtima waliuma uli ngati kupembedza milungu yachabe ndi maula. Popeza inu munakaniza mau a Yehova, Iyenso anakaniza inu, kuti simudzakhalanso mfumu.
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kuchita monga mwa zonyansa za amitundu aja.
Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.
Ndipo pakumva Asa mau awa, ndi chinenero cha Odedi mneneriyo, analimbika mtima, nachotsa zonyansazo m'dziko lonse la Yuda ndi Benjamini, ndi m'mizinda adailanda ku mapiri a Efuremu; nakonza guwa la nsembe la Yehova lokhala pakhomo pachipinda cholowera cha nyumba ya Yehova.
Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho.
Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako, koma wandivuta nazo zonsezi, chifukwa chake taona, Inenso ndidzakubwezera njira yako pamutu pako, ati Ambuye Yehova; ndipo sudzachita choipa ichi choonjezerapo pa zonyansa zako zonse.
Asakhale m'dziko lako iwowa, kuti angakulakwitse pa Ine; pakuti ukatumikira milungu yao, kudzakukhalira msampha ndithu.
Wosocheretsa oongoka mtima alowe m'njira yoipa, adzagwa mwini m'dzenje lake; koma angwiro adzalandira cholowa chabwino.
Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakuti amitundu amene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;
Chifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; chifukwa kuti lilime lao ndi machitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wake. Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.
Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, udzaweruza, udzauweruza mzindawo wa mwazi kodi? Uudziwitse tsono zonyansa zake zonse.
Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.