Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholowa changa chonyansa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo ndinakulowetsani m'dziko la minda, kuti mudye zipatso zake, ndi zabwino zake; koma pamene munalowa, munaipitsa dziko langa, ndi kuyesa cholandira changa chonyansa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Ndidakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma mutangoloŵa m'dzikolo, mudaliipitsa, dziko limene ndidakupatsani mudalisandutsa lonyansa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Ndinakufikitsani ku dziko lachonde kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina. Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:7
28 Mawu Ofanana  

Ndipo analanda mizinda yamalinga, ndi dziko la zonona, nalandira zikhale zaozao nyumba zodzala ndi zokoma zilizonse, zitsime zokumbidwa, minda yampesa, ndi minda ya azitona, ndi mitengo yambiri yazipatso; nadya iwo, nakhuta, nanenepa, nakondwera nako kukoma kwanu kwakukulu.


Koma anakhala osamvera, napandukira Inu, nataya chilamulo chanu m'mbuyo mwao napha aneneri anu akuwachitira umboni, kuwabwezera kwa Inu, nachita zopeputsa zazikulu.


pakuti Yehova wa makamu wadalitsa iwo, ndi kuti, Odalitsika Ejipito anthu anga, ndi Asiriya ntchito ya manja anga, ndi Israele cholowa changa.


Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.


Amati, Ngati mwamuna achotsa mkazi wake, ndipo amchokera iye, nakhala mkazi wa wina, kodi adzabweranso kwa mkaziyo? Dzikolo kodi silidzaipitsidwa? Koma iwe wachita dama ndi mabwenzi ambiri; koma bweranso kwa Ine, ati Yehova.


Kwezera maso ako kumapiri oti see, nuone: sanagone ndi iwe kuti? Panjira wakhalira iwo, monga Mwarabu m'chipululu; ndipo waipitsa dziko ndi zigololo zako, ndi zoipa zako.


Ndipo kunali kuti mbiri ya dama lake inaipitsa dziko, ndipo anachita chigololo ndi miyala ndi mitengo.


ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;


Pakuti ana a Israele ndi ana a Yuda anachita zoipa zokhazokha pamaso panga chiyambire ubwana wao, pakuti ana a Israele anandiputa Ine kokhakokha ndi ntchito ya manja ao, ati Yehova.


popeza sanachite maweruzo anga, koma ananyoza malemba anga, naipsa masabata anga, ndi maso ao anatsata mafano a atate ao.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


tsiku lomwelo ndinawakwezera dzanja langa kuwatulutsa m'dziko la Ejipito, kunka nao kudziko ndinawazondera, moyenda mkaka ndi uchi, ndilo lokometsetsa mwa maiko onse;


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza wandiiwala Ine, ndi kunditaya pambuyo pako, uzisenza iwenso choipa chako ndi zigololo zako.


Wobadwa ndi munthu iwe, muja a nyumba ya Israele anakhala m'dziko mwao, analidetsa ndi njira yao, ndi machitidwe ao; njira yao pamaso panga inanga chidetso cha mkazi amene akusamba.


Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efuremu adzabwerera kunka ku Ejipito; ndipo adzadya chakudya chodetsa mu Asiriya.


Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu.


Ndipo anafotokozera, nati Tinakafika ku dziko limene munatitumirako, ndilo ndithu moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi; ndi zipatso zake siizi.


mtembo wake usakhale pamtengo usiku wonse, koma mumuike ndithu tsiku lomwelo; pakuti wopachikidwa pamtengo atembereredwa ndi Mulungu; kuti mungadetse dziko lanu limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanu.


Pakuti gawo la Yehova ndilo anthu ake; Yakobo ndiye muyeso wa cholowa chake.


Ndipo muzichita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti chikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa