Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 2:8 - Buku Lopatulika

8 Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ansembe sanati, Ali kuti Yehova? Ndi iwo amene agwira malamulo sandidziwa Ine; ndi abusa omwe anandilakwira Ine, ndi aneneri ananenera mwa Baala, natsata zinthu zosapindula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Nawonso ansembe sadafunse kuti, ‘Chauta ali kuti?’ Akatswiri a malamulo sadandidziŵe. Olamulira adandipandukira. Aneneri ankalosa m'dzina la Baala, ndipo ankatsata milungu yachabechabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ansembe nawonso sanafunse kuti, ‘Yehova ali kuti?’ Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe; atsogoleri anandiwukira. Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala, ndi kutsatira mafano achabechabe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 2:8
35 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya ananena ndi anthuwo, Ine ndatsala ndekha mneneri wa Yehova, koma aneneri a Baala ndiwo anthu mazana anai mphambu makumi asanu.


Ndipo kunali, litapendeka dzuwa, ananenera kufikira nthawi ya kupereka nsembe; koma panalibe mau, kapena wovomereza, kapena wakuwamvera.


Ndipo Eliya anati kwa iwo, Gwirani aneneri a Baala, asapulumuke ndi mmodzi yense. Nawagwira, ndipo Eliya anapita nao ku mtsinje wa Kisoni, nawapha pamenepo.


Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga, wakupatsa nyimbo usiku;


Koma iwonso adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali, iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, naphunthwa poweruza.


Pakuti Yehova watsanulira pa inu mzimu wa tulo togonetsa, natseka maso anu, ndiwo aneneri; naphimba mitu yanu, ndiwo alauli.


Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi chitonzo.


Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Ndipo iwo anati, Tiyeni, tilingalire Yeremiya chomchitira choipa; pakuti chilamulo sichidzathera wansembe, kapena uphungu wanzeru, kapena mau mneneri. Tiyeni, timpande iye ndi lilime, tisamvere iye mau ake ali onse.


Kodi mtundu wa anthu unasintha milungu yao, imene siili milungu? Koma anthu anga anasintha ulemerero wao ndi chosapindula.


Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


aneneri anenera monyenga nathandiza ansembe pakulamulira kwao; ndipo anthu anga akonda zotere; ndipo mudzachita chiyani pomalizira pake?


Taonani, mukhulupirira mau onama, osapindulitsa.


koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;


Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.


Wobadwa ndi munthu iwe, Nenera motsutsa abusa a Israele; nenera, nuti nao abusawo, Atero Ambuye Yehova, Tsoka abusa a Israele odzidyetsa okha; kodi abusa sayenera kudyetsa nkhosa?


Anthu anga aonongeka chifukwa cha kusadziwa; popeza unakana kudziwa, Inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga; popeza waiwala chilamulo cha Mulungu wako, Inenso ndidzaiwala ana ako.


Apindulanji nalo fano losema, kuti wakulipanga analisema; fano loyenga ndi mphunzitsi wamabodza, kuti wakulipanga alikhulupirira, atapanga mafano osanena mau?


Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?


Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.


Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwe Atate, kapena Ine.


ndipo inu simunamdziwe Iye; koma Ine ndimdziwa Iye; ndipo ngati ndinena kuti sindimdziwa Iye, ndidzakhala wonama chimodzimodzi inu; koma ndimdziwa Iye, ndipo ndisunga mau ake.


koma takaniza zobisika za manyazi, osayendayenda mochenjerera, kapena kuchita nao mau a Mulungu konyenga; koma ndi maonekedwe a choonadi; tidzivomeretsa tokha ku chikumbumtima cha anthu onse pamaso pa Mulungu.


Adzaphunzitsa Yakobo maweruzo anu, ndi Israele chilamulo chanu; adzaika chofukiza pamaso panu, ndi nsembe yopsereza yamphumphu paguwa la nsembe lanu.


musapatukire inu kutsata zinthu zachabe, zosapindulitsa, zosapulumutsa, popeza zili zopanda pake.


Koma ana a Eli anali oipa; sanadziwe Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa