Yeremiya 2:6 - Buku Lopatulika6 Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Sadalabadeko za Ine Chauta, ngakhale ndine amene ndidaŵatulutsa m'dziko la Aejipito, ndi kuŵatsogolera m'chipululu, m'dziko louma ndi lokumbikakumbika, m'dziko lachilala ndi la mdima wandiweyani, m'dziko limene munthu sadutsamo, kumene sikukhala munthu konse. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti, amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma ndi lokumbikakumbika, mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima, dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’ Onani mutuwo |