Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 12:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 12:11
14 Mawu Ofanana  

Koma izi ndizo uzikonza paguwa la nsembelo; anaankhosa awiri a chaka chimodzi, tsiku ndi tsiku kosalekeza.


Ndipo utatsiriza awa, ugonerenso mbali yako ya kumanja, ndi kusenza mphulupulu ya nyumba ya Yuda; ndakuikira masiku makumi anai, kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi.


Muyesetu anyamata anu masiku khumi; atipatse zomera m'nthaka tidye, ndi madzi timwe.


Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.


Nidzanena mau akutsutsana ndi Wam'mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam'mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthawizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m'dzanja lake mpaka nthawi imodzi, ndi nthawi zina, ndi nthawi yanusu.


Ndipo masomphenya a madzulo ndi mamawa adanenawo ndi oona; koma iwe ubise masomphenyawo, popeza adzachitika atapita masiku ambiri.


Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


Pakuti ana a Israele adzakhala masiku ambiri opanda mfumu, ndi opanda kalonga, ndi opanda nsembe, ndi opanda choimiritsa, ndi opanda efodi kapena aterafi;


Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)


Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:


Ndipo bwalo la kunja kwa Kachisi ulisiye padera, osaliyesa; pakuti adapatsa ilo kwa amitundu; ndipo mzinda wopatulika adzaupondereza miyezi makumi anai mphambu iwiri.


Ndipo mkazi anathawira kuchipululu, kumene ali nayo mbuto yokonzekeratu ndi Mulungu, kuti kumeneko akamdyetse masiku chikwi chimodzi ndi mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.


Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa