Danieli 12:11 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “Kuyambira pamene nsembe ya tsiku ndi tsiku idzathetsedwa ndi kukhazikitsa kwa chonyansa chobweretsa chisokonezo chija, padzapita masiku 1,290. Onani mutuwoBuku Lopatulika11 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai. Onani mutuwo |
Adzachita pangano lolimba ndi anthu ambiri kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Koma pakatinʼpakati pa sabata limodzilo iye adzaletsa kupereka nsembe ndi chopereka. Chonyansa chosakaza chija adzachiyika mʼNyumba ya Mulungu, ndipo chidzakhalapobe mpaka wochita zimenezi atalangidwa ndi chiwonongeko chimene Mulungu ananeneratu.”