Hoseya 9:10 - Buku Lopatulika10 Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndinapeza Israele ngati mphesa m'chipululu, ndinaona makolo anu ngati chipatso choyamba cha mkuyu nyengo yake yoyamba; koma anadza kwa Baala-Peori, nadzipatulira chonyansacho, nasandulika onyansa, chonga chija anachikonda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Chauta akuti, “Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo. Makolo ake aja ndidaŵakondwerera ngati nkhuyu zoyamba kupsa. Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori, ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala. Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo, limene ankalikonda lija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 “Pamene ndinamupeza Israeli zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu. Nditaona makolo anu, zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa. Koma atafika ku Baala Peori, anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho. Onani mutuwo |