Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 9:11 - Buku Lopatulika

11 Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Kunena za Efuremu, ulemerero wao udzauluka ndi kuchoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Ulemerero wa Aefuremu udzaŵathaŵa mouluka ngati mbalame. Sadzabalanso ana. Akazi ao sadzaima, sadzatenga pathupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame. Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 9:11
18 Mawu Ofanana  

Ndipo dzina la wachiwiri anamutcha Efuremu: chifukwa Mulungu anandibalitsa ine m'dziko la kusauka kwanga.


Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.


Ndipo Mikala mwana wamkazi wa Saulo sanaone mwana kufikira tsiku la imfa yake.


Inde, kuunika kwa woipa kudzazima, ndi lawi la moto wake silidzawala.


Apite ngati nkhono yosungunuka; asaone dzuwa monga mtayo.


Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;


Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.


Okhala mu Samariya adzaopera chifanizo cha anaang'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ake adzamva nacho chisoni, ndi ansembe ake amene anakondwera nacho, chifukwa cha ulemerero wake, popeza unachichokera.


Monga anachuluka, momwemo anandichimwira; ndidzasanduliza ulemerero wao ukhale manyazi.


Efuremu adzasanduka bwinja tsiku lakudzudzula; mwa mafuko a Israele ndadziwitsa chodzachitikadi.


Apatseni, Yehova; mudzapatsa chiyani? Muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.


Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za ana a Amoni, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza anatumbula akazi ali m'pakati a Giliyadi, kuti akuze malire ao;


Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.


Zidzakhala zotembereredwa zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.


ndicho chifukwa cha matenda akutuluka pakati pa mapazi ake, ndi ana ake adzawabala; popeza adzawadya m'tseri posowa zinthu zonse; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani mdani wanu m'midzi mwanu.


Woyamba kubadwa wa ng'ombe yake, ulemerero ndi wake; nyanga zake ndizo nyanga zanjati; adzatunga nazo mitundu ya anthu pamodzi, kufikira malekezero a dziko lapansi. Iwo ndiwo zikwi khumi za Efuremu, iwo ndiwo zikwi za Manase.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa