Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 7:30 - Buku Lopatulika

30 Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti alipitse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Chauta akuti, “Anthu a ku Yuda achita zoipa Ine ndikuwona. Aimika mafano ao onyansa m'Nyumba ino imene imadziŵika ndi dzina langa, ndipo aiipitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 “Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:30
20 Mawu Ofanana  

Pakuti anamanganso misanje, imene Hezekiya atate wake adaiononga; nautsira Baala maguwa a nsembe, nasema chifanizo, monga anachita Ahabu mfumu ya Israele, nagwadira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.


Namanga iye maguwa a nsembe m'nyumba ya Yehova imene Yehova adainenera kuti, Mu Yerusalemu ndidzaika dzina langa.


Ndipo anaika chifanizo chosema chimene adachipanga m'nyumba ija Yehova adainenera kwa Davide ndi kwa Solomoni mwana wake kuti, M'nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha mwa mafuko onse a Israele ndidzaikamo dzina langa kosatha.


Ndi maguwa a nsembe anali patsindwi pa chipinda chosanja cha Ahazi adawapanga mafumu a Yuda, ndi maguwa a nsembe adawapanga Manase m'mabwalo awiri a nyumba ya Yehova, mfumu inawagumula, niwachotsa komweko, nitaya fumbi lao ku mtsinje wa Kidroni.


Ndipo anachotsa milungu yachilendo, ndi fanoli m'nyumba ya Yehova, ndi maguwa onse a nsembe anawamanga m'phiri la nyumba ya Yehova ndi mu Yerusalemu, nawataya kunja kwa mzinda.


Pakuti anamanganso misanje adaipasula Hezekiya atate wake, nautsira Abaala maguwa a nsembe, napanga zifanizo, nalambira khamu lonse la kuthambo, nalitumikira.


Ndipo anaika chifanizo chosema cha fanolo adachipanga m'nyumba ya Mulungu, imene Mulungu adati kwa Davide ndi Solomoni mwana wake, M'nyumba muno ndi mu Yerusalemu umene ndausankha m'mafuko onse a Israele ndidzaika dzina langa kunthawi zonse;


Inenso ndidzasankha zodzinyenga nazo, ndipo ndidzatengera mantha ao pa iwo; pakuti pamene ndinaitana, panalibe woyankha; pamene ndinalankhula, iwo sanamve konse; koma anachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene sindinakondwere nacho.


Poyamba ndibwezera mphulupulu yao ndi tchimo lao chowirikiza; chifukwa anaipitsa dziko langa ndi mitembo ya zodetsedwa zao, nadzaza cholowa changa ndi zonyansa zao.


Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.


Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Ndipo chokometsera chake chokongola anachiyesa chodzikuza nacho, napangira mafanizo olaula, ndi zonyansa zao zina; chifukwa chake ndinapatsa ichi chikhale chowadetsa.


Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati padziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.


Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.


Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa