Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 7:31 - Buku Lopatulika

31 Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindiwanauze iwo, sichinalowe m'mtima mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Namanga akachisi a ku Tofeti, kuli m'chigwa cha mwana wa Hinomu, kuti atenthe m'moto ana ao aamuna ndi aakazi; chimene sindinauza iwo, sichinalowa m'mtima mwanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Amanga nsanja yotchedwa Tofeti m'chigwa cha Benihinomu, kuti atenthereko ana ao aamuna ndi aakazi. Zimenezo sindidalamule konse, ngakhale kuziganiza komwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:31
23 Mawu Ofanana  

Napititsa ana ao aamuna ndi aakazi kumoto, naombeza ula, nachita zanyanga, nadzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, kuutsa mkwiyo wake.


Anawaipitsiranso Tofeti, wokhala m'chigwa cha ana a Hinomu; kuti asapitirize mmodzi yense mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pamoto kwa Moleki.


Ndipo anapha ansembe onse a misanje okhalako pa maguwa a nsembe, natentha mafupa a anthu pamenepo, nabwerera kunka ku Yerusalemu.


Nafukizanso yekha m'chigwa cha mwana wa Hinomu, napsereza ana ake m'moto, monga mwa zonyansa za amitundu, amene Yehova anawainga pamaso pa ana a Israele.


Anapititsanso ana ake pamoto m'chigwa cha ana a Hinomu, naombeza maula, nasamalira malodza, nachita zanyanga, naika obwebweta ndi openduza; anachita zoipa zambiri pamaso pa Yehova kuutsa mkwiyo wake.


Pakuti Tofeti wakonzedwa kale, inde chifukwa cha mfumu wakonzedweratu; Iye wazamitsapo, nakuzapo; mulu wakewo ndi moto ndi nkhuni zambiri; mpweya wa Yehova uuyatsa ngati mtsinje wa sulufure.


Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?


nutulukire kuchigwa cha mwana wake wa Hinomu, chimene chili pa khomo la Chipata cha Mapale, nulalikire kumeneko mau amene ndidzakuuza iwe;


Bwanji uti, Sindinaipitsidwe, sindinatsate Abaala? Ona njira yako m'chigwa, dziwa chimene wachichita; ndiwe ngamira yothamanga yoyenda m'njira zake;


Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aidetse.


Ndipo anamanga misanje ya Baala, ili m'chigwa cha mwana wake wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao aamuna ndi aakazi chifukwa cha Moleki; chimene sindinawauze, chimene sichinalowe m'mtima mwanga, kuti achite chonyansa ichi, chochimwitsa Yuda.


Unatenganso ana ako aamuna ndi aakazi amene unandibalirawo, ndi kuwapereka nsembe awathe. Zigololo zako zidachepa kodi,


ndinawadetsanso m'zopereka zao; pakuti anapititsa pamoto onse oyamba kubadwa kuti ndiwapasule; kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo popereka zopereka zanu popititsa ana anu pamoto, mudzidetsa kodi ndi mafano anu onse mpaka lero lino? Ndipo kodi ndidzafunsidwa ndi inu, nyumba ya Israele? Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindidzafunsidwa ndi inu;


Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.


Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga?


Musamatero ndi Yehova Mulungu wanu; pakuti zilizonse zinyansira Yehova, zimene azida Iye, iwowa anazichitira milungu yao; pakuti angakhale ana ao aamuna ndi ana ao aakazi awatentha m'moto, nsembe ya milungu yao.


nakatumikira milungu ina, naigwadira iyo, kapena dzuwa, kapena mwezi, kapena wina wa khamu la kuthambo, losauza Ine;


Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.


nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa