Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Malaki 2:11 - Buku Lopatulika

11 Yuda wachita monyenga, ndi mu Israele ndi mu Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Yuda wachita monyenga, ndi m'Israele ndi m'Yerusalemu mwachitika chonyansa; pakuti Yuda waipsa chipatuliko cha Yehova chimene achikonda, nakwatira mwana wamkazi wa mulungu wachilendo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthu a ku Yuda akhala osakhulupirika, ku Israele ndi ku Yerusalemu akhala akuchita zinthu zonyansa. Anthu a ku Yuda aipitsa Nyumba ya Chauta imene Iye amaikonda. Akhala akukwatira akazi opembedza milungu yachikunja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo.

Onani mutuwo Koperani




Malaki 2:11
27 Mawu Ofanana  

Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.


Chifukwa chake tsono, musamapereka ana anu akazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna ana ao akazi, kapena kufuna mtendere wao ndi kukoma kwao nthawi yonse, kuti mukhale olimba, ndi kudya zokoma za m'dziko, ndi kulisiyira ana anu cholowa cha kunthawi yonse.


Ndipo anadziphatikiza ndi Baala-Peori, nadyanso nsembe za akufa.


Israele anali wopatulikira Yehova, zipatso zoyamba za zopindula zake; onse amene adzamudya iye adzayesedwa opalamula; choipa chidzawagwera, ati Yehova.


Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.


ndi kudza ndi kuima pamaso panga m'nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ndi kuti, Talanditsidwa; kuti muchite zonyansa izi?


napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.


Ndipo wina anachita chonyansa ndi mkazi wa mnansi wake, winanso wadetsa mpongozi wake mwamanyazi, ndi wina mwa iwe anaipitsa mlongo wake mwana wamkazi wa atate wake.


Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga.


Ndipo muzikhala oyera kwa Ine; pakuti Ine Yehova ndine woyera, ndipo ndinakusiyanitsani kwa mitundu ya anthu mukhale anga.


Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.


Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


nakwatira ana aakazi a iwowa, napereka ana ao akazi kwa ana aamuna a iwowa natumikira milungu yao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa