Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 6:10 - Buku Lopatulika

10 M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pakati pa Aisraele ndaonapo zinthu zonyansa. Aefuremu adachita zadama, Aisraele adadziipitsa pakupembedza mafano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndaona chinthu choopsa kwambiri mʼnyumba ya Israeli. Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere, ndipo Israeli wadzidetsa.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 6:10
14 Mawu Ofanana  

Koma iye analeka uphungu wa mandodawo, umene anampangirawo, nakafunsira kwa achinyamata anzake oimirira pamaso pake,


chifukwa cha machimo a Yerobowamu, amene adachimwa nao, nachimwitsa nao Aisraele, ndi kuutsa kwake kumene anaputa nako mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israele.


Kudatero, popeza ana a Israele adachimwira Yehova Mulungu wao, amene anawakweza kuwatulutsa m'dziko la Ejipito pansi padzanja la Farao mfumu ya Aejipito, ndipo anaopa milungu ina,


Chifukwa chake atero Yehova; Funsanitu m'mitundu, ndani wamva zotero; namwali wa Israele wachita chinthu choopsetsa kwambiri.


Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndinaona chinthu choopsetsa; achita chigololo, ayenda monama, alimbitsa manja a ochita zoipa, ndipo palibe wobwerera kuleka zoipa zake; onse akhala kwa Ine ngati Sodomu, ndi okhalamo ake ngati Gomora.


Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.


Koma Ohola anachita chigololo pamene anali wanga, anaumirira mabwenzi ake Aasiriya oyandikizana naye;


Ndipo anachita nao zigololo zake, ndiwo anthu osankhika a ku Asiriya onsewo, ndipo ali onse anawaumirira anadziipsa nao mafano ao.


Chigololo, ndi vinyo, ndi vinyo watsopano, zichotsa mtima.


Anthu anga afunsira kumtengo wao, ndi ndodo yao iwafotokozera; pakuti mzimu wachigololo wawalakwitsa, ndipo achita chigololo kuchokera Mulungu wao.


Efuremu waphatikana ndi mafano, mlekeni.


Ndimdziwa Efuremu, ndi Israele sandibisikira; pakuti Efuremu iwe, wachita uhule tsopano, Israele wadetsedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa