Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 13:27 - Buku Lopatulika

27 Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndaona zonyansa zako, ndi zigololo zako, ndi zakumemesa zako, ndi chinyerinyeri cha dama lako, pamapiri ndi m'munda. Tsoka kwa iwe, Yerusalemu! Sudzayeretsedwa; kodi zidzatero mpaka liti?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Ndaona zonyansa zanu, zigololo zanu, kutchetcherera kwanu, ndi ziwerewere zanu zochitika pa mapiri, kuthengo. Tsoka kwa inu a ku Yerusalemu! Mudzakhala osayeretsedwabe pa zachipembedzo mpaka liti?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu ndi ziwerewere zanu, zochitika pa mapiri ndi mʼminda. Tsoka iwe Yerusalemu! Udzakhala wosayeretsedwa pa zachipembedzo mpaka liti?”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 13:27
32 Mawu Ofanana  

Anena mau, alankhula zowawa; adzitamandira onse ochita zopanda pake.


Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


Pamwamba paphiri lalitalitali unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.


zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao.


Wokondedwa wanga afunanji m'nyumba mwanga, popeza wachita choipa ndi ambiri, ndipo thupi lopatulika lakuchokera iwe? Pamene uchita choipa ukondwera nacho.


Ndipo Yehova anati kwa ine masiku a Yosiya mfumu, Kodi waona chimene wachichita Israele, wobwerera m'mbuyo? Wakwera pa mapiri aatali onse, ndi patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndi kuchita dama pamenepo.


Ndipo kudachitika utatha zoipa zako zonse, (tsoka iwe, tsoka, ati Ambuye Yehova)


naufunyulula pamaso panga; ndipo unalembedwa m'kati ndi kubwalo; munalembedwa m'mwemo nyimbo za maliro, ndi chisoni, ndi tsoka.


Nditafika nao m'dzikolo ndinawakwezera dzanja langa kuwapatsa ilo, anapenya chitunda chilichonse chachitali, ndi mtengo uliwonse wagudugudu, naphera pomwepo nsembe zao, naperekapo nsembe zao zondiputa, aponso anachita fungo lao lokoma, nathiraponso nsembe zao zothira.


Ntchito ya mphika ndi yolemetsa, koma dzimbiri lake lalikulu siliuchokera, dzimbiri lake liyenera kumoto.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Tsoka mzinda wokhetsa mwazi, mphika m'mene muli dzimbiri, losauchokera dzimbiri lake; uchotsemo chiwalochiwalo; sanaugwere maere.


Ndipo ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera; ndidzakuyeretsani kukuchotserani zodetsa zanu zonse, ndi mafano anu nonse.


Atero Ambuye Yehova, Ichi chomwe adzandipempha a nyumba ya Israele ndiwachitire ichi, ndidzawachulukitsira anthu ngati nkhosa.


Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pokhala ophedwa ao pakati pa mafano ao, pozinga maguwa ao a nsembe, pa zitunda zonse zazitali, pamwamba pa mapiri onse, ndi patsinde pa mitengo yogudira yonse, ndi patsinde pa thundu aliyense wagudugudu, pomwe adapereka zonunkhira zokoma kwa mafano ao onse.


Chiyambi cha kunena kwa Yehova mwa Hoseya. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wachigololo ndi ana achigololo; pakuti dziko latsata chigololo chokhachokha kuleka kutsata Yehova.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Mwanawang'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?


Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mzinda wozunza!


Tsoka kwa iwe, Korazini! Tsoka kwa iwe, Betsaida! Chifukwa ngati zamphamvu zimene zachitidwa mwa inu zikadachitidwa mu Tiro ndi mu Sidoni, akadatembenuka mtima kalekale m'ziguduli ndi m'phulusa.


kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.


Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Ndipo ndinaona, ndipo ndinamva chiombankhanga chilikuuluka pakati pamwamba, ndi kunena ndi mau aakulu, Tsoka, tsoka, tsoka, iwo akukhala padziko, chifukwa cha mau otsala a lipenga la angelo atatu asanaombe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa