Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 73:27 - Buku Lopatulika

27 Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Iwo amene ali kutali ndi Inu adzawonongeka; Inu mumawononga onse osakhulupirika pamaso panu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 73:27
15 Mawu Ofanana  

Momwemo Saulo anafa, chifukwa cha kulakwa kwake analakwira Yehova, kulakwira mau a Yehova amene sanawasunge; ndiponso chifukwa cha kufunsira wobwebweta, kufunsirako,


Natumiza iye makalata kwa Ayuda onse, kumaiko zana limodzi mphambu makumi awiri kudza asanu ndi awiri a ufumu wa Ahasuwero, ndiwo mau a mtendere ndi choonadi;


Ndipo anadziipsa nazo ntchito zao, nachita chigololo nao machitidwe ao.


Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu.


ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;


Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;


Inu Mwabzala iwo, inde, anagwiritsatu mizu; amera, inde, abalatu zipatso; muli pafupi m'kamwa mwao, muli patali ndi impso zao.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;


Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.


ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa