Yeremiya 8:12 - Buku Lopatulika12 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati? Iyai, sankachita manyazi mpang'ono pomwe. Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe. Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao amene adagwa kale. Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga,” akutero Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi? Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe; iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe. Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale; adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga, akutero Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo padzakhala monga ndi anthu, moteronso ndi ansembe; monga ndi mtumiki, moteronso ndi mbuyake; monga ndi mdzakazi, moteronso ndi mbuyake wamkazi; monga ndi wogula, moteronso ndi wogulitsa; monga ndi wobwereka, moteronso ndi wombwereka; monga ndi wotenga phindu, moteronso ndi wombwezera phindu kwa iye.