Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 8:13 - Buku Lopatulika

13 Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 “Ndidzaŵatheratu. Ndidzachotsa dzinthu dza m'minda mwao. Sipadzakhala mphesa pa mpesa, kapena nkhuyu pa mkuyu, ndi masamba ake omwe adzauma. Zinthu zimene ndidaŵapatsa, ndidzaŵachotsera zonse.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “ ‘Ndidzatenga zokolola zawo, Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa kapena nkhuyu pa mkuyu, ndipo masamba ake adzawuma. Zinthu zimene ndinawapatsa ndidzawachotsera.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 8:13
25 Mawu Ofanana  

Chifukwa kuti munda wampesa wa madera khumi udzangobala bati imodzi ya vinyo, ndi mbeu za maefa khumi zidzangobala efa imodzi.


Pamene asala chakudya, sindidzamva kufuula kwao; ndipo pamene apereka nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa sindidzawalandira; koma ndidzawatha ndi lupanga, ndi chilala, ndi mliri.


Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatume, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa.


Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.


Adzadya zokolola zako, ndi mkate wako, umene ana ako aamuna ndi aakazi ayenera kudya; adzadya nkhosa zako ndi zoweta zako; adzadya mphesa zako ndi nkhuyu zako; adzapasula ndi lupanga mizinda yamalinga yako, imene ukhulupiriramo.


Chifukwa chake, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pamalo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.


Chifukwa chake ndinawatsanulira ukali wanga, ndawatha ndi moto wa kuzaza kwanga, njira yaoyao ndinaibweza pamutu pao, ati Ambuye Yehova.


Ndipo ndidzapasula mipesa yake ndi mikuyu yake, imene adanena, Iyi ndi mphotho yanga anandipatsa ondikondawo; ndipo ndidzaisandutsa thengo, ndi nyama zakuthengo zidzaidya.


Unaonongadi mpesa wanga, nunyenya mkuyu wanga, nukungudza konse, nuutaya; nthambi zake zasanduka zotumbuluka.


ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.


Chinkana mkuyu suphuka, kungakhale kulibe zipatso kumpesa; yalephera ntchito ya azitona, ndi m'minda m'mosapatsa chakudya; ndi zoweta zachotsedwa kukhola, palibenso ng'ombe m'makola mwao;


Ndipo ndinaitana chilala chidzere dziko, ndi mapiri, ndi tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zimene ibala nthaka, ndi anthu, ndi zoweta, ndi ntchito zonse za manja.


Ndinakukanthani ndi chinsikwi ndi chinoni ndi matalala m'ntchito zonse za manja anu, koma simunabwerere kudza kwa Ine, ati Yehova.


Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m'munda, ati Yehova wa makamu.


Ndipo pakuona mkuyu umodzi panjira, anafika pamenepo, napeza palibe kanthu koma masamba okhaokha; nati Iye kwa uwo, Sudzabalanso chipatso kunthawi zonse. Ndipo pomwepo mkuyuwo unafota.


Pakuti latuluka dzuwa ndi kutentha kwake, ndipo laumitsa udzu; ndipo lathothoka duwa lake, ndi ukoma wa maonekedwe ake waonongeka; koteronso wachuma adzafota m'mayendedwe ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa