Baibulo limatiuza kuti Mulungu amaona kutali munthu wodzikuza. Kudzikuza ndi khalidwe lomwe silikondweretsa Mulungu, ndipo limapezeka mwa anthu ambiri, kumawapangitsa kudzidalira mopambanitsa ndikuganiza kuti angathe kulamulira chilichonse. Munthu wodzikuza sadziwa zolakwa zake, koma nthawi zonse amaona zolakwa za anzake, n’kunyalanyaza zake.
Njira yokha yothawa mtima umenewu womwe umawononga maganizo ndi mtima wanu, ndikuvomereza Mulungu pa chilichonse chimene muchita. Muziwerama pamaso pake ndi kuvomereza kuti mumadalira Iye, osati mphamvu kapena luso lanu. Koma chifukwa cha chikondi ndi chisomo chake. Ndikukutsimikizirani kuti mukachita izi, chikondi chake chochiritsa chidzakuphimbani, chidzasintha maganizo anu, ndi kukupangani munthu watsopano m’chifaniziro chake.
Dzipumbitsitseni pansi pa dzanja lamphamvu la Yehova, ndipo nthawi yake ikadzakwana adzakukwezani ndi kukuyikani pamalo amene anakukonzerani kuyambira kalekale.
Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Chitsiriziro cha kanthu chiposa chiyambi chake; wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima. Usakangaze mumtima mwako kukwiya; pakuti mkwiyo ugona m'chifuwa cha zitsiru.
Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.
Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza. Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.
Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.
Taonani, nditsutsana nawe, wonyada iwe, ati Ambuye, Yehova wa makamu; pakuti tsiku lako lafika, nthawi imene ndidzakulanga iwe.
nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima,
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Apo afuula, koma Iye sawayankha; chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oipa. Zedi Mulungu samvera zachabe, ndi Wamphamvuyonse sazisamalira.
Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera; nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.
Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto; ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.
Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye; kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga; musamakwezetsa nyanga yanu; musamalankhula ndi khosi louma.
Achita ufumu mwa mphamvu yake kosatha; maso ake ayang'anira amitundu; opikisana ndi Iye asadzikuze.
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?
Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsa nzeru zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi, ndakuika pamaso pa mafumu, kuti akupenye.
Chifukwa padzakhala tsiku la Yehova wa makamu pa zonse zonyada ndi zakudzikuza, ndi pa zonse zotukulidwa; ndipo zidzatsitsidwa;
Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.
Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.
Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala: Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.
Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.
Chabwino; iwo anathyoledwa ndi kusakhulupirira kwao, ndipo iwe umaima ndi chikhulupiriro chako. Usamadzikuza mumtima, koma opatu:
Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
Inde, amanga akatundu olemera ndi osautsa ponyamula, nawasenza pa mapewa a anthu; koma iwo eni okha safuna kuwasuntha amenewo ndi chala chao.
Anena mau, alankhula zowawa; adzitamandira onse ochita zopanda pake. Aphwanya anthu anu, Yehova, nazunza cholowa chanu.
Yehova, mtima wanga sunadzikuze ndi maso anga sanakwezeke; ndipo sindinatsate zazikulu, kapena zodabwitsa zondiposa. Indedi, ndinalinganiza ndi kutontholetsa moyo wanga; ngati mwana womletsa kuyamwa amake, moyo wanga ndili nao ngati mwana womletsa kuyamwa.
Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziononga wekha? Usapambanitse kuipa, ngakhale kupusa; uferenji nthawi yako isanafike?
Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu. Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona.
Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.
Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.
Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.
Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro. Pakuti monga m'thupi limodzi tili nazo ziwalo zambiri, ndipo ziwalo zonsezo sizili nayo ntchito imodzimodzi; chomwecho ife, ndife ambiri, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndi ziwalo zinzake, wina ndi wina.
Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.
Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.
Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.
Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.