Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 59:12 - Buku Lopatulika

12 Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo chifukwa cha mawu a milomo yawo, iwo akodwe mʼkunyada kwawo. Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 59:12
20 Mawu Ofanana  

Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao, nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.


Podzikuza woipa apsereza waumphawi; agwe m'chiwembu anapanganacho.


M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.


Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.


Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.


M'kulakwa kwa milomo muli msampha woipa; koma wolungama amatuluka m'mavuto.


M'kamwa mwa wopusa mumuononga, milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.


wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako, wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.


milomo ya akutsutsana nane ndi zolingalira zao za pa ine tsiku lonse.


Koma ndidzawasiya owerengeka apulumuke lupanga, ndi njala, ndi mliri, kuti afotokoze zonyansa zao kwa amitundu kumene afikako; ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Koma kulumbira, ndi kunama, ndi kupha, ndi kuba, ndi kuchita chigololo; aboola, ndi mwazi ukhudzana nao mwazi.


Tsiku ilo sudzachita manyazi ndi zochita zako zonse unandilakwira nazo; pakuti pamenepo ndidzachotsa pakati pako amene akondwera ndi kudzikuza kwako, ndipo sudzachita kudzikuzanso m'phiri langa lopatulika.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


nanena, Mfumu, takumbukira ife kuti wonyenga uja anati, pamene anali ndi moyo, Ndidzauka pofika masiku atatu.


Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa