Masalimo 59:13 - Buku Lopatulika13 Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza mu Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Muwathe mumkwiyo, muwagulule psiti. Ndipo adziwe kuti Mulungu ndiye woweruza m'Yakobo, kufikira malekezero a dziko la pansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 muwawononge mu ukali (wanu) muwawononge mpaka atheretu. Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi kuti Mulungu amalamulira Yakobo. Onani mutuwo |
kuti adzakuingitsani kukuchotsani kwa anthu, ndi pokhala panu padzakhala pamodzi ndi nyama zakuthengo; ndipo mudzadya udzu ngati ng'ombe, nimudzakhala wokhathamira ndi mame a kumwamba, ndipo zidzakupitirani nthawi zisanu ndi ziwiri, mpaka mudzadziwa kuti Wam'mwambamwamba alamulira mu ufumu wa anthu, naupereka kwa aliyense Iye afuna mwini.