Miyambo 4 - Buku LopatulikaChenjezo lakuti afune Nzeru nalewe njira za oipa 1 Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha; 2 pakuti ndikuphunzitsani zabwino; musasiye chilangizo changa. 3 Pakuti ndinali mwana kwa atate wanga, wokondedwa ndi mai, ndine ndekha, sanabale wina. 4 Atate nandiphunzitsa, nati kwa ine, mtima wako uumirire mau anga; sunga malamulo anga, nukhale ndi moyo. 5 Tenga nzeru, tenga luntha; usaiwale, usapatuke pa mau a m'kamwa mwanga; 6 usasiye nzeru, ndipo idzakusunga; uikonde, idzakutchinjiriza. 7 Nzeru ipambana, tatenga nzeru; m'kutenga kwako konseko utenge luntha. 8 Uilemekeze, ndipo idzakukweza; idzakutengera ulemu pamene uifungatira. 9 Idzaika chisada cha chisomo pamutu pako; idzakupatsa korona wokongola. 10 Tamvera mwananga, nulandire mau anga; ndipo zaka za moyo wako zidzachuluka. 11 Ndakuphunzitsa m'njira ya nzeru, ndakuyendetsa m'mayendedwe olungama. 12 Mapazi ako sadzaombana ulikuyenda; ukathamanga, sudzaphunthwa. 13 Gwira mwambo, osauleka; uusunge; pakuti ndiwo moyo wako. 14 Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. 15 Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire. 16 Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera. 17 Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba. 18 Koma mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbee. 19 Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa. 20 Mwananga, tamvera mau anga; tcherera makutu ku zonena zanga. 21 Asachoke kumaso ako; uwasunge m'kati mwa mtima wako. 22 Pakuti ali moyo kwa omwe awapeza, nalamitsa thupi lao lonse. 23 Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo. 24 Tasiya m'kamwa mokhota, uike patali milomo yopotoka. 25 Maso ako ayang'ane m'tsogolo, zikope zako zipenye moongoka. 26 Sinkhasinkha bwino mayendedwe a mapazi ako; njira zako zonse zikonzeke. 27 Usapatuke kudzanja lamanja kapena kulamanzere; suntha phazi lako kusiya zoipa. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi