Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 34:16 - Buku Lopatulika

16 Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa, kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 34:16
15 Mawu Ofanana  

Chikumbukiro chake chidzatayika m'dziko, ndipo adzasowa dzina kukhwalala.


Sawachotsera wolungama maso ake, koma pamodzi ndi mafumu pa mpando wao awakhazika chikhazikire, ndipo akwezeka.


Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya; aonongeka amitundu m'dziko lake.


Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi, ndi maziko a mapiri ananjenjemera nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.


Taonani, diso la Yehova lili pa iwo akumuopa Iye, pa iwo akuyembekeza chifundo chake.


Kodi Iye wakupanga khutu ngwosamva? Kodi Iye wakuumba diso ngwosapenya?


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.


Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Taonani, ndidzayang'anitsa nkhope yanga pa inu ndikuchitireni inu choipa, ndidule Yuda yense.


Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Angakhale alowa ndende pamaso pa adani ao, kumeneko ndidzalamulira lupanga, ndipo lidzawapha; ndipo ndidzayang'anitsa maso anga kwa iwowa, kuwachitira choipa, si chokoma ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa