Mawu oti “chilakolako cha uchimo” amatanthauza kufunitsitsa kwambiri zosangalatsa. M’malemba ambiri a m’Baibulo, mawuwa amalumikizidwa ndi kugonjera ku chibadwa cha uchimo pa zinthu zosiyanasiyana m’moyo wathu. Nthawi zambiri chilakolako cha uchimo chimalumikizidwa ndi zilakolako za kugonana, ndipo chimaonedwa ngati chimodzi mwa zinthu zazikulu zomwe chimawonekera. Komabe, chingatanthauzenso kufunitsitsa kwambiri chuma ndi zosangalatsa za padziko lapansi, kapena kugonjera ku zilakolako zosalamulirika.
Ukangolandira Yesu mumtima mwako, sudzalimbananso wekha, chifukwa iye amapereka chisomo choti uchite zinthu m’mphamvu zake pa zimene sungakwanitse wekha, monga momwe Baibulo limanenera pa Afilipi 4:13, “Ndingathe kuchita zonse mwa Khristu amene amandipatsa mphamvu.” Suli wekha, ukapereka zofooka zako zonse kwa Yesu, iye adzakuzikitsa m’moyo wako, ndikukupatsa mphamvu zake kuti upambane choipa.
Ndikofunikira kufunafuna nkhope ya Mulungu tsiku lililonse kuti tikhale moyo wogwirizana ndi chifuniro chake osati zilakolako zosokoneza za thupi. Njira yokhayo yopambana chilakolako cha uchimo ndi kulola Yesu kukhala Ambuye wa moyo wako, ndikumulola kuti akusinthe mkati mwako ndikukupanga kukhala cholengedwa chatsopano.
Ndikofunikira kukumbukira kuti m’mawu ake muli chakudya, ndipo kudzera mwa iwo timalandira malangizo oti tizitha kupirira nthawi zovuta.
Koma ndinena, Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi sizilingana; kuti zimene muzifuna musazichite.
Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.
koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi;
Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha:
Pakuti mwa iwo akhala akukwawira m'nyumba, nagwira akazi opusa, osenza akatundu a zoipa zao, otengedwa nazo zilakolako za mitundumitundu:
Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo;
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha. Kapena simudziwa kuti thupi lanu lili Kachisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tochepachepa? Pakuti munagulidwa ndi mtengo wake wapatali; chifukwa chake lemekezani Mulungu m'thupi lanu.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
amene ife tonsenso tinagonera pakati pao kale, m'zilakolako za thupi lathu, ndi kuchita zifuniro za thupi, ndi za maganizo, ndipo tinali ana a mkwiyo chibadwire, monganso otsalawo;
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;
Koma thawa zilakolako za unyamata, nutsate chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, pamodzi ndi iwo akuitana pa Ambuye ndi mitima yoyera.
ndi kutiphunzitsa ife kuti, pokana chisapembedzo ndi zilakolako za dziko lapansi, tikhale ndi moyo m'dziko lino odziletsa, ndi olungama, ndi opembedza;
Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.
Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama; yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang'ana mkazi kumkhumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.
kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo; koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu, nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.
Asakuchititse kaso m'mtima mwako, asakukole ndi zikope zake. Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.
koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;
Zichokera kuti nkhondo, zichokera kuti zolimbana mwa inu? Kodi sizichokera kuzikhumbitso zanu zochita nkhondo m'ziwalo zanu? Dzichepetseni pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani? Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti. Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa. Potero kwa iye amene adziwa kuchita bwino, ndipo sachita, kwa iye kuli tchimo. Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simungathe kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi; amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen. Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi: pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwe ao a chibadwidwe akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzinso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi cholakalaka chao wina ndi mnzake, amuna okhaokha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao.
kuti nthawi yotsalira simukakhalenso ndi moyo m'thupi kutsata zilakolako za anthu, koma chifuniro cha Mulungu. Pakuti nthawi yapitayi idakufikirani kuchita chifuniro cha amitundu, poyendayenda inu m'kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, maimwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka;
Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; pakuti tili ziwalo za thupi lake. Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna. kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko. Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa; ndi kuwalonjeza ufulu, pamene iwo eni ali akapolo a chivundi; pakuti chimene munthu agonjetsedwa nacho, adzakhala kapolo wa chimenecho.
pakuti ngati mukhala ndi moyo monga mwa thupi, mudzafa; koma ngati ndi mzimu mufetsa zochita zake za thupi, mudzakhala ndi moyo.
Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthawi yonse.
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Mtima wako usapatukire kunjira ya mkaziyo, usasochere m'mayendedwe ake. Pakuti amagwetsa ambiri, atawalasa; ndipo ophedwa ndi iye achulukadi. Nyumba yake ndiyo njira ya kumanda, yotsikira kuzipinda za imfa.
Tavalani zida zonse za Mulungu, kuti mudzakhoze kuchilimika pokana machenjerero a mdierekezi. Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu, Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake. Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondweretsa, komatu chowawa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloweretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo. Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka; ndipo lambulani miseu yolunjika yoyendamo mapazi anu, kuti chotsimphinacho chisapatulidwe m'njira, koma chichiritsidwe. Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye: ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao; kuti pangakhale wachigololo, kapena wamnyozo, ngati Esau, amene anagulitsa ukulu wake wobadwa nao mtanda umodzi wa chakudya. Pakuti mudziwa kutinso pamene anafuna kulowa dalitsolo, anakanidwa (pakuti sanapeze malo akulapa), angakhale analifunafuna ndi misozi. Pakuti simunayandikire phiri lokhudzika, ndi lakupsa moto, ndi pakuda bii, ndi mdima, ndi namondwe, ndi mau a lipenga, ndi manenedwe a mau, manenedwe amene iwo adamvawo anapempha kuti asawaonjezerepo mau; Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.
Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.
monga ana omvera osadzifanizitsanso ndi zilakolako zakale, pokhala osadziwa inu; komatu monga Iye wakuitana inu ali woyera mtima, khalani inunso oyera mtima m'makhalidwe anu onse; popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.
Popeza mphamvu ya umulungu wake idatipatsa ife zonse za pamoyo ndi chipembedzo, mwa chidziwitso cha Iye amene adatiitana ife ndi ulemerero ndi ukoma wake wa Iye yekha; mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.
Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera. M'chikondano cha anzanu wina ndi mnzake mukondane ndi chikondi chenicheni; mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu; musakhale aulesi m'machitidwe anu; khalani achangu mumzimu, tumikirani Ambuye; kondwerani m'chiyembekezo, pirirani m'masautso; limbikani chilimbikire m'kupemphera. Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo. Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere. Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira. Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha. Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye. Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.
Pamenepo Yesu anatengedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira. Pomwepo mdierekezi anamsiya Iye, ndipo onani, angelo anadza, namtumikira Iye.
Pakuti adakuitanani inu, abale, mukhale mfulu; chokhacho musachite nao ufulu wanu chothandizira thupi, komatu mwachikondi chitiranani ukapolo.
koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.
Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao, Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse. Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi; kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu; kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu. Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa; koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu; kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi. Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao, odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao; amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo. ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
Pakuti ndidziwa kuti m'kati mwanga, ndiko m'thupi langa, simukhala chinthu chabwino; pakuti kufuna ndili nako, koma kuchita chabwino sindikupeza. Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita. Pakuti mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamunayo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamunayo. Koma ngati ndichita chimene sindichifuna, si ndinenso amene ndichichita, koma uchimo wakukhalabe m'kati mwanga ndiwo.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai.
Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma. Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
Ndipo yense wakukhala nacho chiyembekezo ichi pa Iye, adziyeretsa yekha, monga Iyeyu ali Woyera.
podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupilo la uchimo likaonongedwe, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo; pakuti iye amene anafa anamasulidwa kuuchimo.
Chezerani ndi kupemphera, kuti mungalowe m'kuyesedwa: mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye.
Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.
Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.
Khristu anatisandutsa mfulu, kuti tikhale mfulu; chifukwa chake chilimikani, musakodwenso ndi goli la ukapolo.
Chilungamo cha oongoka mtima chidzawapulumutsa; koma achiwembu adzagwidwa ndi mphulupulu yao.
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m'mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake.
Koma ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losaponyedwa thupi lako lonse mu Gehena. Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba. Ndipo ngati dzanja lako lamanja likulakwitsa iwe, ulidule, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe kuti chimodzi cha ziwalo zako chionongeke, losamuka thupi lako lonse ku Gehena.
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire: ameneyo mumkanize okhazikika m'chikhulupiriro, podziwa kuti zowawa zomwezo zilimkukwaniridwa pa abale anu ali m'dziko.
Kodi simudziwa kuti muli Kachisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu? Ngati wina aononga Kachisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti Kachisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.
Inu, tsono, okondedwa, pozizindikiratu izi, chenjerani, kuti potengedwa ndi kulakwa kwa iwo osaweruzika, mungagwe kusiya chikhazikiko chanu. Koma kulani m'chisomo ndi chizindikiritso cha Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu; kwa Iye kukhale ulemerero, tsopano ndi nthawi zonse. Amen.
woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.
Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.
kuti mukakhale osalakwa ndi oona, ana a Mulungu opanda chilema pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka, mwa iwo amene muonekera monga mauniko m'dziko lapansi,
yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu, kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;
Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.
Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka mu ntchito ya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse, inu amene kale simunali anthu, koma tsopano muli anthu a Mulungu; amene kale simunalandire chifundo, koma tsopano mwalandira chifundo. Okondedwa, ndikudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo; ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira. Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, chifukwa cha Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse; kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ochita zoipa, koma kusimba ochita zabwino. Pakuti chifuniro cha Mulungu chitere, kuti ndi kuchita zabwino mukatontholetse chipulukiro cha anthu opusa; monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga chobisira choipa, koma ngati akapolo a Mulungu. Chitirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Chitirani mfumu ulemu. Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali. Pakuti ichi ndi chisomo ngati munthu, chifukwa cha chikumbumtima pa Mulungu alola zachisoni, pakumva zowawa wosaziyenera. lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nao kufikira chipulumutso; Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pochimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pochita zabwino, ndi kumvako ndiko chisomo pa Mulungu. Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Khristu anamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake; amene sanachite tchimo, ndipo m'kamwa mwake sichinapezedwa chinyengo; amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama; amene anasenza machimo athu mwini yekha m'thupi mwake pamtanda, kuti ife, titafa kumachimo, tikakhale ndi moyo kutsata chilungamo; ameneyo mikwingwirima yake munachiritsidwa nayo. Pakuti munalikusochera ngati nkhosa; koma tsopano mwabwera kwa Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu. ngati mwalawa kuti Ambuye ali wokoma mtima;
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.
Koma inu simuli m'thupi ai, koma mumzimu, ngatitu Mzimu wa Mulungu akhalabe mwa inu. Koma ngati munthu alibe Mzimu wa Khristu, siali wake wa Khristu.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa; sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi; chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine. Pakuti iye amene afuna kupulumutsa moyo wake adzautaya: koma iye amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine, adzaupeza. Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?
ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi.
Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.
Pakuti ife tonse tiyenera kuonetsedwa kumpando wakuweruza wa Khristu, kuti yense alandire zochitika m'thupi, monga momwe anachita, kapena chabwino kapena choipa.
Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.
Abale, ine sindiwerengera ndekha kuti ndatha kuchigwira: koma chinthu chimodzi ndichichita; poiwaladi zam'mbuyo, ndi kutambalitsira zam'tsogolo, ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu a mwa Khristu Yesu.