Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Ahebri 13:18 - Buku Lopatulika

18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbumtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mutipempherere ife; pakuti takopeka mtima kuti tili nacho chikumbu mtima chokoma m'zonse, pofuna kukhala nao makhalidwe abwino.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Muzitipempherera ifeyo, pakuti sitipeneka konse kuti tili ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndipo tatsimikiza kuchita zonse mwachilungamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Mutipempherere ifenso. Pakuti tikutsimikiza kuti tili ndi chikumbumtima changwiro ndipo timafuna kuchita zinthu zonse mwaulemu.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 13:18
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m'bwalo la akulu a milandu anati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.


M'menemonso ndidziyesera ndekha ndikhale nacho nthawi zonse chikumbumtima chosanditsutsa cha kwa Mulungu ndi kwa anthu.


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m'madyerero ndi kuledzera ai, si m'chigololo ndi chonyansa ai, si mu ndeu ndi nkhwidzi ai.


Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Chotsalira, abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zolemekezeka, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zokongola, zilizonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.


ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,


kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.


Abale, tipempherereni ife.


Chotsalira, abale, mutipempherere, kuti mau a Ambuye athamange, nalemekezedwe, monganso kwanu;


koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.


chimenenso chifaniziro chake chikupulumutsani tsopano, ndicho ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lake la thupi, komatu funso lake la chikumbumtima chokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Khristu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa