Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yohane 17:17 - Buku Lopatulika

17 Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Patulani iwo m'choonadi; mau anu ndi choonadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Muziŵapatula ndi mau anu kuti akhale anthu anu. Mau anuwo ngoona zedi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi.

Onani mutuwo Koperani




Yohane 17:17
23 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munalonjezana ndi mnyamata wanu kumchitira chabwino ichi,


Malangizo anu andizindikiritsa; chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.


Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga, kuti ndisalakwire Inu.


Mboni zanu ndizo zolungama kosatha; mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.


Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.


Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji? Akawasamalira monga mwa mau anu.


Mau a Yehova ndi mau oona; ngati siliva woyenga m'ng'anjo yadothi, yoiyeretsa kasanu ndi kawiri.


Koma fanizoli litere: Mbeuzo ndizo mau a Mulungu.


Ndipo zija za m'nthaka yokoma, ndiwo amene anamva mau nawasunga mu mtima woona ndi wabwino, nabala zipatso ndi kupirira.


Mwakhala okonzeka tsopano inu chifukwa cha mau amene ndalankhula ndi inu.


Ndipo chifukwa cha iwo Ine ndidzipatula ndekha kuti iwonso akhale opatulidwa m'choonadi.


ndipo mudzazindikira choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.


Koma tsopano mufuna kundipha Ine, ndine munthu amene ndinalankhula ndi inu choonadi, chimene ndinamva kwa Mulungu; ichi Abrahamu sanachite.


ndipo sanalekanitse ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m'chikhulupiriro.


Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa Ambuye, tisandulika m'chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero kunka kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa Ambuye Mzimu.


ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;


kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mau;


Koma tiyenera ife tiziyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu, abale okondedwa ndi Ambuye, kuti Mulungu anakusankhani inu kuyambira pachiyambi, mulandire chipulumutso mwa chiyeretso cha Mzimu ndi chikhulupiriro cha choonadi;


Mwa ichi, mutavula chinyanso chonse ndi chisefukiro cha choipa, landirani ndi chifatso mau ookedwa mwa inu, okhoza kupulumutsa moyo wanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa