Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 7:24 - Buku Lopatulika

24 Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Koma anthuwo sadamvere, sadasamaleko, ndipo adapitirira kukhala osamvera ndi mitima yao yoipa. Adayang'ana zam'mbuyo osati zakutsogolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:24
37 Mawu Ofanana  

ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.


Ha! Akadandimvera anthu anga, akadayenda m'njira zanga Israele!


Anthu oipa awa, amene akana kumva mau anga, amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wao, atsata milungu ina kuitumikira, ndi kuigwadira, adzakhala ngati mpango uwu, wosayenera kanthu.


Pakuti monga mpango uthina m'chuuno cha munthu, chomwecho ndinathinitsa kwa Ine nyumba yonse ya Israele ndi nyumba yonse ya Yuda, ati Yehova, kuti akhale kwa Ine anthu, ndi dzina, ndi chilemekezo, ndi ulemerero; koma anakana kumva.


Iwe wandikana Ine, ati Yehova, wabwerera m'mbuyo; chifukwa chake ndatambasulira dzanja langa pa iwe, ndi kukuononga iwe; ndatopa ndi kulekerera.


ndipo mwachita zoipa zopambana makolo anu; pakuti, taonani, muyenda yense potsata kuumirira kwa mtima wake woipa, kuti musandimvere Ine;


koma sanamvere, sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao, kuti asamve asalandire langizo.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


koma ukachita choipa pamaso panga, osamvera mau anga, pamenepo ndidzaleka chabwinocho, ndidati ndiwachitire.


Koma iwo ati, Palibe chiyembekezero; pakuti ife tidzatsata zilingaliro zathu, ndipo tidzachita yense monga mwa kuuma kwa mtima wake woipa.


amene ati kwa mtengo, Iwe ndiwe atate wanga; ndi kwa mwala, Wandibala; pakuti anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope yao; koma m'nthawi ya kuvutidwa kwao adzati, Ukani, tipulumutseni.


Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvere mau anga.


Anena chinenere kwa iwo akundinyoza Ine, ati Yehova, Mudzakhala ndi mtendere; ndipo kwa yense amene ayenda m'kuumirira kwa mtima wake amati, Palibe choipa chidzagwera inu.


Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.


Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.


ndipo analowa, nakhalamo; koma sanamvere mau anu, sanayende m'chilamulo chanu; sanachite kanthu ka zonse zimene munawauza achite; chifukwa chake mwafikitsa pa iwo choipa chonsechi;


Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvere kulangizidwa.


Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yake yoipa, konzani machitidwe anu, musatsate milungu ina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunanditchere khutu lanu, simunandimvere Ine.


Yehova atero, Imani m'njira ndi kuona, funsani za mayendedwe akale, m'menemo muli njira yabwino, muyende m'menemo, ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu; koma anati, Sitidzayendamo.


koma sanandimvere Ine sanatchere khutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.


Bwanji abwerera anthu awa a Yerusalemu chibwererere? Agwiritsa chinyengo, akana kubwera.


koma anatsata kuuma kwa mtima wao, ndi Baala, monga makolo ao anawaphunzitsa;


Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.


popeza ananyoza maweruzo anga, osayenda m'malemba anga, naipsa masabata anga; pakuti mitima yao inatsata mafano ao.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


Koma anapandukira Ine, osafuna kundimvera Ine, sanataye yense zonyansa pamaso pake, sanaleke mafano a Ejipito; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'dziko la Ejipito.


sitinamvere atumiki anu aneneri, amene ananena m'dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m'dziko.


Adzachitengeranso ku Asiriya chikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efuremu adzatenga manyazi, ndi Israele adzachita manyazi ndi uphungu wake.


Pakuti Israele wachita kuuma khosi ngati ng'ombe yaikazi yaing'ono youma khosi; tsopano Yehova adzawadyetsa ngati mwanawankhosa kuthengo lalikulu.


Pakuti asunga malemba a Omuri, ndi ntchito za nyumba ya Ahabu, ndipo mumayenda mu uphungu wao; kuti ndikusandulize bwinja, ndi okhalamo chotsonya; ndipo mudzasenza chitonzo cha anthu anga.


Koma anakana kumvera, nakaniza phewa lao, natseka makutu ao, kuti asamve.


Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwake, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa