Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, Mulungu amasankha zinthu zofooka ndi zonyozeka padziko lapansi, zinthu zomwe anthu amaziona ngati zopanda pake, kuti azitsitse zamphamvu. Izi zimachitika kuti pasakhale munthu wodzitamandira pamaso pa Mulungu.
Tsiku lililonse tiyenera kuzindikira kuti timafunikira Mulungu ndipo timadalira chikondi chake chosatha. Munthu wodzitamandira ndi amene amaganiza kuti angathe kuchita chilichonse yekha, akudalira luso lake ndi mphamvu zake.
Mulungu amafuna kuti ana ake akhale opanda kudzitamandira chifukwa iye amatsutsa odzikuza, koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa. Akamadza mtima wakudzitamandira, kumbukira momwe unalili poyamba, Mulungu asanalowe m'moyo mwako. Uone zabwino zonse zomwe wakuchitira.
Perekani ulemerero wonse kwa Yehova, chifukwa poyamba munali mumdima, koma tsopano kuwala kwakukulu kwawala m'moyo mwanu. Choncho, musadzitamandire pa chilichonse chifukwa zonse zomwe muli nazo ndi zomwe muli, ndi chifukwa cha chisomo chachikulu chomwe Mulungu wakupatsani.
Musalankhulenso modzikuza kwambiri motero; m'kamwa mwanu musatuluke zolulutsa; chifukwa Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo Iye ayesa zochita anthu.
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.
Pamenepo kudzitama kuli kuti? Kwaletsedwa. Ndi lamulo lotani? La ntchito kodi? Iai; koma ndi lamulo la chikhulupiriro.
Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.
ndipo zopanda pake za dziko lapansi, ndi zonyozeka, anazisankhula Mulungu, ndi zinthu zoti kulibe; kuti akathere zinthu zoti ziliko; kuti thupi lililonse lisadzitamande pamaso pa Mulungu.
Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.
Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi.
osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira,
Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.
Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.
Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo?
Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.
Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.
Atero Yehova, wanzeru asadzitamandire m'nzeru zake, wamphamvu asadzitamandire m'mphamvu yake, wachuma asadzitamandire m'chuma chake;
Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
Pakuti ngati Abrahamu anayesedwa wolungama chifukwa cha ntchito, iye akhala nacho chodzitamandira; koma kulinga kwa Mulungu ai.
Koma yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.
Ndipo mfumu ya Israele anayankha, nati, Kamuuzeni, Wakumanga zida asadzikuze ngati wakuvulayo.
Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.
Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa.
Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumtsata m'mbuyo.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza,
Pakuti muli opulumutsidwa ndi chisomo chakuchita mwa chikhulupiriro, ndipo ichi chosachokera kwa inu: chili mphatso ya Mulungu; chosachokera kuntchito, kuti asadzitamandire munthu aliyense.
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;
Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
Kudzikuza kwa munthu kudzamchepetsa; koma wokhala ndi mtima wodzichepetsa adzalemekezedwa.
Yehova wa makamu wapanga uphungu uwu, kuipitsa kunyada kwa ulemerero wonse, kupepula onse olemekezeka a m'dziko lapansi.
Chomwecho muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.
Pakuti akusiyanitsa iwe ndani? Ndipo uli nacho chiyani chosati wachilandira? Koma ngati wachilandira udzitamanda bwanji, monga ngati sunachilandire?
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka. Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa. Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri. Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba.
Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.
Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.
Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?
Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;
iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye; kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.
Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
Musaweruze, kuti mungaweruzidwe. Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi? Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye? Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri. Lowani pa chipata chopapatiza; chifukwa chipata chili chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka. Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa. Mudzawazindikira ndi zipatso zao. Kodi atchera mphesa paminga, kapena nkhuyu pamtula? Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma. Mtengo uliwonse wosapatsa chipatso chokoma, audula, nautaya kumoto. Pakuti ndi kuweruza kumene muweruza nako, inunso mudzaweruzidwa; ndipo ndi muyeso umene muyesa nao, kudzayesedwa kwa inunso.
Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,
Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.
Tsiku lonse atenderuza mau anga, zolingirira zao zonse zili pa ine kundichitira choipa.
Ndipo amati, Yehova sachipenya, ndi Mulungu wa Yakobo sachisamalira. Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?
nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba. Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole. Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa. Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine; kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni? Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse. Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu. Chifukwa chake yense amene adzichepetsa yekha monga kamwana aka, yemweyo ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba.
Ndani iwe wakuweruza mnyamata wa mwini wake? Iye aimirira kapena kugwa kwa mbuye wake wa mwini yekha. Ndipo adzaimiritsidwa; pakuti Ambuye ali wamphamvu kumuimiritsa.
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
Pakuti zonsezi mkono wanga wazilenga, momwemo zonsezi zinaoneka, ati Yehova; koma ndidzayang'anira munthu uyu amene ali waumphawi, ndi wa mzimu wosweka, nanthunthumira ndi mau anga.
Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.
Usadzitame pamaso pa mfumu, ngakhale kuima m'malo mwa akulu. Pakuti kunena kwa iwe, Takwera kuno, kupambana ndi kuti utsitsidwe pamaso pa kalonga, amene maso ako anamuona.
Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.
Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.
Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje, nakonda malo a ulemu pamaphwando, ndi mipando ya ulemu m'masunagoge, ndi kulonjeredwa m'misika, ndi kutchedwa ndi anthu, Rabi.
Udzitamandiranji ndi choipa, chiphona iwe? Chifundo cha Mulungu chikhala tsiku lonse. Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga. Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo,
komatu dandaulirananani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo;
Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.
Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira. Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.
Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma. Ukani molungama, ndipo musachimwe; pakuti ena alibe chidziwitso cha Mulungu. Ndilankhula kunyaza inu.
Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera; pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.
Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.