Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 75:4 - Buku Lopatulika

4 Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndinati kwa odzitamandira, musamachita zodzitamandira; ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndimauza anthu odzitama kuti, “Musadzitame,” ndiponso anthu oipa kuti, “Musadzitukumule chifukwa cha mphamvu zanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 75:4
12 Mawu Ofanana  

Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake, chilemekezo cha okondedwa ake onse; ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye. Aleluya.


Koma olungama akondwere; atumphe ndi chimwemwe pamaso pa Mulungu; ndipo asekere nacho chikondwerero.


Popeza Inu ndinu ulemerero wa mphamvu yao; ndipo potivomereza Inu nyanga yathu idzakwezeka.


Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.


Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?


Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;


Lekani, achibwana inu, nimukhale ndi moyo; nimuyende m'njira ya nzeru.


Pamenepo ndinati, Adzeranji awa? Ndipo ananena, nati, Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda, wopandanso wina woweramutsa mutu wake; koma awa anadza kuziopsa, kugwetsa nyanga za amitundu, amene anakwezera dziko la Yuda nyanga zao kulimwaza.


Amuutsa waumphawi m'fumbi, nanyamula wosowa padzala, kukamkhalitsa kwa akalonga; ndi kuti akhale nacho cholowa cha chimpando cha ulemerero. Chifukwa nsanamira za dziko lapansi nza Yehova, ndipo Iye anakhazika dziko pa izo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa