Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa mu ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo ananena kwa ine, Chisomo changa chikukwanira; pakuti mphamvu yanga ithedwa m'ufooko. Chifukwa chake makamaka ndidzadzitamandira mokondweratu m'mafooko anga, kuti mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:9
38 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anampenya ana a aneneri okhala ku Yeriko pandunji pake, anati, Mzimu wa Eliya watera pa Elisa. Ndipo anadza kukomana naye, nadziweramitsa pansi kumaso kwake.


M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu, chifukwa cha otsutsana ndi Inu, kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.


Ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Yehova Mulungu wako ali pakati pako, wamphamvu wakupulumutsa; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala wopanda thamo m'chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.


Ndipo Yesu anadza nalankhula nao, nanena, Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.


ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.


Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


Koma ndi chisomo cha Mulungu ndili ine amene ndili; ndipo chisomo chake cha kwa ine sichinakhale chopanda pake, koma ndinagwirira ntchito yochuluka ya iwo onse; koma si ine, koma chisomo cha Mulungu chakukhala ndi ine.


Ndipo ine ndinakhala nanu mofooka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.


kuti chikhulupiriro chanu chisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.


Ngati ndiyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira ndi za kufooka kwanga.


Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza kumasomphenya ndi mavumbulutso a Ambuye.


Chifukwa chake ndisangalala m'mafooko, m'ziwawa, m'zikakamizo, m'mazunzo, m'zipsinjiko, chifukwa cha Khristu; pakuti pamene ndifooka, pamenepo ndili wamphamvu.


Ndipo ndidzapereka ndi kuperekedwa konse chifukwa cha miyoyo yanu mokondweratu. Ngati ndikonda inu kochuluka koposa, kodi ndikondedwa kochepa?


Chifukwa cha wotereyo ndidzadzitamandira; koma chifukwa cha ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m'zofooka zanga.


kuti monga mwa chuma cha ulemerero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu,


Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.


olimbikitsidwa m'chilimbiko chonse, monga mwa mphamvu ya ulemerero wake, kuchitira chipiriro chonse ndi kuleza mtima konse pamodzi ndi chimwemwe,


koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa.


Kodi sindinakulamulire iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kulikonse umukako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa