Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 10:12 - Buku Lopatulika

12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 10:12
10 Mawu Ofanana  

Zoonadi inu ndinu anthu, ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.


Kudya uchi wambiri sikuli kwabwino; chomwecho kufunafuna ulemu wakowako sikuli ulemu.


Kodi uona munthu wodziyesa wanzeru? Ngakhale chitsiru chidzachenjera koma ameneyo ai.


Wina akutume, si m'kamwa mwako ai; mlendo, si milomo ya iwe wekha.


Mfarisiyo anaimirira napemphera izi mwa yekha, Mulungu, ndikuyamikani kuti sindili monga anthu onse ena, opambapamba, osalungama, achigololo, kapenanso monga wamsonkho uyu;


Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,


Woteroyo ayese ichi kuti monga tili ife ndi mau mwa makalata, pokhala palibe ife, tili oterenso m'machitidwe pokhala tili pomwepo.


pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.


Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu?


Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa