Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 10:13 - Buku Lopatulika

13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Koma ife sitidzadzitamandira popitirira muyeso, koma monga mwa muyeso wa chilekezero chimene Mulungu anatigawira muyeso, kufikira ngakhale kwa inunso.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Kunena za ife, sitinganyade mopitirira malire. Tidzasamala malire omwe Mulungu adatiikira potifikitsa mpaka kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 10:13
12 Mawu Ofanana  

Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,


Monga mitambo ndi mphepo popanda mvula, momwemo ndiye wodzikweza ndi zipatso zake monyenga.


Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.


Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye.


Koma ine nditi, Sanamva iwo kodi! Indetu, Liu lao linatulukira kudziko lonse lapansi, ndi maneno ao ku malekezero a dziko lokhalamo anthu.


Pakuti ndi chisomo chapatsidwa kwa ine, ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha, monga Mulungu anagawira kwa munthu aliyense muyeso wa chikhulupiriro.


Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;


ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.


Koma zonse izi achita Mzimu mmodzi yemweyo, nagawira yense pa yekha monga afuna.


Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu.


monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa