Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 5:6 - Buku Lopatulika

6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Pamenepo palibe choti inu nkunyadira ai. Kodi simuŵadziŵa mau aja akuti, “Chofufumitsira buledi chapang'ono chimafufumitsa mkate wonse?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kudziwa kwanu si kwabwino. Kodi simukudziwa kuti yisiti wochepa amafufumitsa mphumphu yaufa wonse wa tirigu?

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 5:6
12 Mawu Ofanana  

Achigololo onsewo; akunga ng'anjo anaitenthetsa wootcha mkate; aleka kusonkha moto, poyambira kukanda mtanda kufikira watupa mtandawo.


Fanizo lina ananena kwa iwo; Ufumu wa Kumwamba uli wofanafana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anachitenga, nachibisa m'miyeso itatu ya ufa, kufikira wonse unatupa.


Ufanana ndi chotupitsa mikate, chimene mkazi anatenga, nachibisa mu miyeso itatu ya ufa, kufikira unatupo wonsewo.


Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Chifukwa chake palibe mmodzi adzitamande mwa anthu. Pakuti zinthu zonse nzanu;


Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.


Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse.


ndipo mau ao adzanyeka chilonda; a iwo ali Himeneo ndi Fileto;


Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa