Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 5:5 - Buku Lopatulika

5 kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 mumupereke munthuyu kwa Satana, kuti chikhalidwe chake cha uchimo chiwonongedwe ndikuti mzimu wake udzapulumuke pa tsiku la Ambuye.

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 5:5
23 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Satana, Taona, akhale m'dzanja lako; moyo wake wokha uuleke.


Muike munthu woipa akhale mkulu wake; ndi mdani aime padzanja lamanja lake.


Udzammenya ndi nthyole, nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.


Koma wansembe akachiona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sichinakumbe kubzola khungu, koma chazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;


Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.


Simoni, Simoni, taona, Satana anafunsa akutengeni kuti akupeteni ngati tirigu;


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


amenenso adzakukhazikitsani inu kufikira chimaliziro, kuti mukhale opanda chifukwa m'tsiku la Ambuye wathu Yesu Khristu.


Koma poweruzidwa, tilangidwa ndi Ambuye, kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi dziko lapansi.


koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.


ndi kukhala okonzeka kubwezera chilango kusamvera konse, pamene kumvera kwanu kudzakwaniridwa.


Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, chifukwa cha ukulu woposa wa mavumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelo wa Satana kuti anditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.


Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa.


pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;


a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.


(Ambuye ampatse iye apeze chifundo ndi Ambuye tsiku lijalo); ndi muja ananditumikira m'zinthu zambiri mu Efeso, uzindikira iwe bwino.


akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu, m'menemo miyamba potentha moto idzakanganuka, ndi zam'mwamba zidzasungunuka ndi kutentha kwakukulu.


Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa