Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yakobo 1:19 - Buku Lopatulika

19 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima.

Onani mutuwo Koperani




Yakobo 1:19
54 Mawu Ofanana  

Anawerenganso m'buku la chilamulo cha Mulungu tsiku ndi tsiku, kuyambira tsiku loyamba kufikira tsiku lotsiriza. Nachita chikondwerero masiku asanu ndi awiri; ndi tsiku lachisanu ndi chitatu ndilo msonkhano woletsa, monga mwa malemba.


nakana kumvera, osakumbukiranso zodabwitsa zanu munazichita pakati pao; koma anaumitsa khosi lao, ndipo m'kupanduka kwao anaika mtsogoleri abwerere kunka ku ukapolo wao; koma Inu ndinu Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo; ndipo simunawasiye.


Naimirira poima pao, nawerenga m'buku la chilamulo cha Yehova Mulungu wao limodzi la magawo anai a tsiku; ndi limodzi la magawo anai anawulula, napembedza Yehova Mulungu wao.


Kodi ndidzangolindira popeza sanena iwo, popeza akhala duu osayankhanso?


Pochuluka mau zolakwa sizisoweka; koma wokhala chete achita mwanzeru.


Wogwira pakamwa pake asunga moyo wake; koma woyasamula milomo yake adzaonongeka.


Wokangaza kukwiya adzachita utsiru; ndipo munthu wa ziwembu adzadedwa.


Wosakwiya msanga apambana kumvetsa; koma wansontho akuza utsiru.


Munthu wozaza aputa makani; koma wosakwiya msanga atonthoza makangano.


Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziwa; koma m'kamwa mwa opusa mutsanulira utsiru.


Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mzinda.


Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.


Wopanda chikamwakamwa apambana kudziwa; ndipo wofatsa mtima ali wanzeru.


Wobwezera mau asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.


Munthu waukali alipire mwini; pakuti ukampulumutsa udzateronso.


Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake asunga moyo wake kumavuto.


Wosalamulira mtima wake akunga mzinda wopasuka wopanda linga.


Kodi uona munthu wansontho m'mau ake? Ngakhale chitsiru chidzachenjera, koma ameneyo ai.


Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.


Davide mwini yekha amtchula Iye Ambuye; ndipo ali mwana wake bwanji? Ndipo anthu a makamuwo anakondwa kumva Iye.


Ndipo ambiri anaunjikana, kotero kuti anasowa malo, ngakhale pakhomo pomwe; ndipo analankhula nao mau.


Koma amisonkho onse ndi anthu ochimwa analikumyandikira kudzamva Iye.


ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.


Ndipo m'masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),


Pamenepo ndinatumiza kwa inu osachedwa; ndipo mwachita bwino mwadza kuno. Chifukwa chake taonani tilitonse pano pamaso pa Mulungu, kumva zonse Ambuye anakulamulirani.


Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.


Amenewa anali mfulu koposa a mu Tesalonika, popeza analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m'malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.


Ndipo anali chikhalire m'chiphunzitso cha atumwi ndi m'chiyanjano, m'kunyema mkate ndi mapemphero.


Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,


Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.


Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.


Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:


Ndipo mwa ichinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandire monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso achita mwa inu okhulupirira.


Musanyengedwe, abale anga okondedwa.


Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu;


Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.


Abale anga, pakuti muli nacho chikhulupiriro cha Ambuye wathu Yesu Khristu, Ambuye wa ulemerero, musakhale okondera ndi kusamala maonekedwe.


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.


Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.


Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro.


Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake;


Sindinakulembereni chifukwa simudziwa choonadi, koma chifukwa muchidziwa, ndi chifukwa kulibe bodza lochokera kwa choonadi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa