2 Akorinto 10:15 - Buku Lopatulika15 osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira, Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201415 osadzitamandira popitirira muyeso mwa machititso a ena; koma tili nacho chiyembekezo kuti pakukula chikhulupiriro chanu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa chilekezero chathu kwa kuchulukira, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa15 Motero sitinyadira ntchito zimene anthu ena adazigwira m'dera limene Mulungu adatiikira ife. Kwenikweni tikuyembekeza kuti chikhulupiriro chanu chidzakula, ndipo kuti ntchito yathunso pakati panu idzakula, koma osabzola malire a dera lathu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero15 Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri, Onani mutuwo |