Masalimo 64 - Buku LopatulikaDavide apempha Mulungu amtchinjirize pa omlalira Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga; sungani moyo wanga angandiopse mdani. 2 Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake. 3 Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa; 4 kuponyera wangwiro mobisika: Amponyera modzidzimutsa, osaopa. 5 Alimbikitsana m'chinthu choipa; apangana za kutchera misampha mobisika; akuti, Adzaiona ndani? 6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama. 7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa. 8 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa. 9 Ndipo anthu onse adzachita mantha; nadzabukitsa chochita Mulungu, nadzasamalira ntchito yake. 10 Wolungama adzakondwera mwa Yehova, nadzakhulupirira Iye; ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi