Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 64:6 - Buku Lopatulika

6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha; chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Amaganizira zoipa nkumati, “Takonza mochenjera ndithu chiwembu chathu.” Malingaliro ndi zofuna za mtima wa munthu nzobisika.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati, “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!” Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 64:6
16 Mawu Ofanana  

ndipo panali pamene iye anamva kuti ndinakweza mau anga ndi kufuula, iye anasiya chofunda chake kwa ine nathawira kubwalo.


Anena m'mtima mwake, Mulungu waiwala; wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.


Mboni za chiwawa ziuka, zindifunsa zosadziwa ine.


Mumtima mwao ayesa kuti nyumba zao zikhala chikhalire, ndi mokhala iwo ku mibadwomibadwo; atchapo dzina lao padziko pao.


Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.


Uphungu wa m'mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.


Tsoka kwa iwo amene afunitsa kubisira Yehova uphungu wao, ndi ntchito zao zili mumdima, ndipo amati ndani ationa ife? Ndani atidziwa ife?


Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wonama wakutsutsa Yesu, kuti amuphe Iye;


Ayuda anamyankha iye, Tili nacho chilamulo ife, ndipo monga mwa chilamulocho ayenera kufa, chifukwa anadziyesera Mwana wa Mulungu.


Chifukwa chake musaweruze kanthu isanadze nthawi yake, kufikira akadze Ambuye, amenenso adzaonetsera zobisika za mdima, nadzasonyeza zitsimikizo za mtima; ndipo pamenepo yense adzakhala nao uyamiko wake wa kwa Mulungu.


Pamenepo Doegi wa ku Edomu, anaimirira ndi anyamata a Saulo, nayankha, nati, Ine ndinamuona mwana wa Yeseyo alikufika ku Nobu, kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi.


Davide nanena ndi Saulo, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukuchitirani choipa.


Koma Nabala anayankha anyamata a Davide nati, Davide ndani? Ndi mwana wa Yese ndani? Masiku ano pali anyamata ambiri akungotaya ambuye ao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa