Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 64:7 - Buku Lopatulika

7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Koma Mulungu adzaŵaponya mivi. Motero mwadzidzidzi iwo adzalasidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi; mwadzidzidzi adzakanthidwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 64:7
18 Mawu Ofanana  

Ndipo munthu anakoka uta wake chiponyeponye, nalasa mfumu ya Israele pakati pa maluma a malaya achitsulo; tsono ananena ndi mnyamata wa galeta wake, Tembenuza dzanja lako, nundichotse kunkhondo, popeza ndalasidwa.


Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa, mzimu wanga uwumwa ulembe wake; zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.


Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa; inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.


kuponyera wangwiro mobisika: Amponyera modzidzimutsa, osaopa.


Ha? M'kamphindi ayesedwa bwinja; athedwa konse ndi zoopsa.


Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.


Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


chifukwa chake kuipa kumeneku kudzakhala kwa inu monga pogumuka pofuna kugwa, monga potukuka m'khoma lalitali, kugumuka kwake kufika modzidzimutsa dzidzidzi.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Pomwepo adzakhala awiri m'munda; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa:


Ndidzawaunjikira zoipa; ndidzawathera mivi yanga.


Mivi yanga ndiiledzeretsa nao mwazi, ndi lupanga langa lidzalusira nyama; ndi mwazi wa ophedwa ndi ogwidwa, ndi mutu wachitsitsi wa mdani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa