Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 64:4 - Buku Lopatulika

4 kuponyera wangwiro mobisika: Amponyera modzidzimutsa, osaopa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 kuponyera wangwiro mobisika: Amponyera modzidzimutsa, osaopa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Amabisalira anthu osalakwa namaŵalasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa; amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 64:4
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena nao anyamata ake onse akukhala naye ku Yerusalemu, Nyamukani tithawe, tikapanda kuthawa palibe mmodzi wa ife adzapulumuka Abisalomu; fulumirani kuchoka, angatipeze msanga ndi kutigwetsera zoipa ndi kukantha mzinda ndi lupanga lakuthwa.


Nati adani athu, Sadzadziwa kapena kuona mpaka talowa pakati pao, ndi kuwapha, ndi kuleketsa ntchitoyi.


Pakuti, onani, oipa akoka uta, apiringidza muvi wao pansinga, kuwaponyera mumdima oongoka mtima.


Mulungu adzamva, nadzawasautsa, ndiye wokhalabe chiyambire kale lomwe. Popeza iwowa sasinthika konse, ndipo saopa Mulungu.


Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza, nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.


Mukwezeke m'mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba padziko lonse lapansi.


Koma Mulungu adzawaponyera muvi; adzalaswa modzidzimutsa.


Munapyoza ndi maluti ake mutu wa ankhondo ake; anadza ngati kamvulumvulu kundimwaza; kukondwerera kwao kunanga kufuna kutha ozunzika mobisika.


Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.


Ndipo Saulo anaponya mkondowo; pakuti anati, Ndidzapyoza Davide ndi kumphatikiza ndi khoma. Ndipo Davide analewa kawiri kuchoka pamaso pake.


Ndipo Saulo anayesa kupyoza Davide kumphatikiza kukhoma ndi mkondowo; koma iye anadzilanditsa kuchoka pamaso pa Saulo; ndipo analasa khoma; ndipo Davide anathawa napulumuka usiku uja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa