Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 34:21 - Buku Lopatulika

21 Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Choyipa chidzapha anthu oyipa; adani a olungama adzapezeka olakwa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 34:21
22 Mawu Ofanana  

Ndipo inafa mfumu, naifikitsa ku Samariya, naika mfumu mu Samariya.


Ndipo mfumu ya Israele inati kwa Yehosafati, Alipo munthu wina kuti tifunsire kwa Yehova mwa iye; koma ndimuda, popeza samanenera za ine zabwino, koma zoipa; ndiye Mikaya mwana wake wa Imila. Nati Yehosafati, Isamatero mfumu.


Iwowa anagonjeka, nagwa; koma ife tauka, ndipo takhala chilili.


Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede.


Ndipo ndidzaphwanya omsautsa pamaso pake; ndidzapandanso odana naye.


Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.


Audye m'nyumba imodzi; usatulukira nayo kubwalo nyama ina; ndipo musathyole fupa lake.


Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.


Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka.


Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.


Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Dziko lapansi silingathe kudana ndi inu; koma Ine lindida popeza Ine ndilichitira umboni, kuti ntchito zake zili zoipa.


popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso,


amene adzamva chilango, ndicho chionongeko chosatha chowasiyanitsa kunkhope ya Ambuye, ndi kuulemerero wa mphamvu yake,


Tsono Saulo ananena ndi wonyamula zida zake, Solola lupanga lako, undipyoze nalo; kuti osadulidwa awa angabwere ndi kundipyoza, ndi kundiseka. Koma wonyamula zida zake anakana; chifukwa anaopa ndithu. Chifukwa chake Saulo anatenga lupanga lake naligwera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa