Pa moyo wanga, ndidzakumana ndi zinthu zosangalatsa, komanso zinthu zomwe zidzandibweretsera chisoni ndi mphwayi. Yesu, munthu wangwiro komanso wabwino kwambiri amene anakhalapo padziko lapansi, anakumananso ndi mavuto ambiri: anabeledwa, anapsinjidwa, anakana ndi kunyozedwa. Komabe, palibe chilichonse mwa izi chomwe chinasintha chikondi chake pa anthu. M'malo motittemberera, anatikonda ndi chikondi chosatha ndipo anapempha Atate kuti atikhululukire machimo athu.
Ndikofunika kukumbukira kuti anthu ambiri adzayesa kukupwetekani ndi kukuvutitsani, komanso kukusetsani, maloto anu kapena ntchito zanu. Nthawi zina mungafooke mtima ndi kufuna kungotayika chifukwa cha manyazi. Komabe, ndikukulemberani izi lero kuti ndikulimbikitseni. Ngakhale ena angakusekeni, ndikofunika kwambiri kudziwa zomwe Mulungu amaganiza za inu. Kwa iye, ndinu cholengedwa chodabwitsa, ndipo Mawu ake amati: "Ndithudi adzaseka onyoza, koma odzichepetsa adzawapatsa chisomo." (Miyambo 3:34).
Musadandaule ndi zomwe ena akunena kapena kuchita. Mulungu sadzamasula wolakwa. Khulupirirani Mawu ake, pumulani mwa Iye ndipo mulole dzanja lake lamphamvu likutetezeni ku onse akuzunzani. Musagonje ku chiwembu cha mdani chokuopsezani; kumbukirani kuti zonse mukhoza mwa Khristu amene akukupatsani mphamvu, ndipo m'dzina lake muli opambana.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru? Tembenukani pamene ndikudzudzulani; taonani, nditsanulira pa inu mzimu wanga, ndikudziwitsani mau anga.
Kodi mudzakonda zazibwana kufikira liti, achibwana inu? Onyoza ndi kukonda kunyoza, opusa ndi kuda nzeru?
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.
Yehova, mwandikopa ine, ndipo ndinakopedwa; muli ndi mphamvu koposa ine, ndipo mwapambana; ine ndikhala choseketsa dzuwa lonse, onse andiseka.
Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.
ndi kuyamba kuchizindikira ichi kuti masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni,
Woweruza munthu wonyoza adzichititsa yekha manyazi; yemwe adzudzula wochimwa angodetsa mbiri yakeyake. Usadzudzule wonyoza kuti angakude; dzudzula wanzeru adzakukonda.
Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.
Ndipo pamene Yesu analikukwera ku Yerusalemu, anatenga ophunzira khumi ndi awiri napita nao pa okha, ndipo panjira anati kwa iwo, Onani, tikwera ku Yerusalemu; ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi, ndipo iwo adzamweruza kuti ayenera imfa, nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.
Ndipo anadzitengera khumi ndi awiriwo, nati kwa iwo, Taonani, tikwera kunka ku Yerusalemu, ndipo zidzakwaniritsidwa kwa Mwana wa Munthu zonse zolembedwa ndi aneneri.
Koma tsopano iwo osafikana msinkhu wanga andiseka, iwo amene atate ao ndikadawapeputsa, osawaika pamodzi ndi agalu olinda nkhosa zanga.
Ndipo amuna amene analikusunga Yesu anamnyoza Iye, nampanda. Ndipo anamkulunga Iye m'maso, namfunsa, nati, Talota; anakupanda Iwe ndani? Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano.
Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha. Atsike tsopano pamtanda, Khristu mfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.
Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.
Menya wonyoza, ndipo achibwana adzachenjera; nudzudzule wozindikira adzazindikira nzeru.
Wochitira chiphwete aumphawi atonza Mlengi; wokondwera ndi tsoka sadzapulumuka chilango.
Diso lochitira atate wake chiphwete, ndi kunyoza kumvera amake, makwangwala a kumtsinje adzalikolowola, ana a mphungu adzalidya.
Mboni yopanda pake inyoza chiweruzo; m'kamwa mwa amphulupulu mumeza zoipa. Akonzera onyoza chiweruzo, ndi mikwingwirima pamsana pa opusa.
Pakuti kuseka kwa chitsiru kunga minga ilikuthetheka pansi pa mphika; ichinso ndi chabe.
Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.
kuti ananena nanu, Pa nthawi yotsiriza padzakhala otonza, akuyenda monga mwa zilakolako zosapembedza za iwo okha.
Wodala munthuyo wosayenda mu uphungu wa oipa, kapena wosaimirira m'njira ya ochimwa, kapena wosakhala pansi pa bwalo la onyoza.
Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.
Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza.
Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga, koma uku kunandikhalira chotonza. Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi. Okhala pachipata akamba za ine; ndipo oledzera andiimba.
Chikoti chiyenera kavalo, ndi cham'kamwa chiyenera bulu, ndi nthyole iyenera pamsana pa zitsiru.
Usayankhe chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti ungafanane nacho iwe wekha. Yankha chitsiru monga mwa utsiru wake, kuti asadziyese wanzeru.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Ndipo analuka korona waminga, namveka pamutu pake, namgwiritsa bango m'dzanja lamanja lake; ndipo anagwada pansi pamaso pake, namchitira chipongwe, nati, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!
Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!
Odala inu, pamene anthu adzada inu, nadzapatula inu, nadzatonza inu, nadzalitaya dzina lanu monga loipa, chifukwa cha Mwana wa Munthu.
Koma iwe uweruziranji mbale wako? Kapena iwenso upeputsiranji mbale wako? Pakuti ife tonse tidzaimirira kumpando wakuweruza wa Mulungu.
Pakuti mau a mtanda ali ndithu chinthu chopusa kwa iwo akutayika, koma kwa ife amene tilikupulumutsidwa ali mphamvu ya Mulungu.
Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.
Koma ngati Khristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanji kuti kulibe kuuka kwa akufa? Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Khristunso sanaukitsidwe; ndipo ngati Khristu sanaukitsidwe kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanunso chili chabe.
Musanyengedwe; Mulungu sanyozeka; pakuti chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza. Woika lamulo ndi woweruza ndiye mmodzi, ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuononga; koma iwe woweruza mnzako ndiwe yani?
Mutisandutsa chotonza kwa anzathu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga. Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu, ndi kuti anthu atipukusire mitu.
Pakamwa pao achimwa ndi mau onse a pa milomo yao, potero akodwe m'kudzitamandira kwao, ndiponso chifukwa cha kutemberera ndi bodza azilankhula.
Ndipo chovala changa ndinayesa chiguduli, koma amandiphera mwambi. Okhala pachipata akamba za ine; ndipo oledzera andiimba.
Usapangire mnzako chiwembu; popeza akhala nawe pafupi osatekeseka. Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa.
Milomo ya wopusa ifikitsa makangano; ndipo m'kamwa mwake muputa kukwapulidwa. M'kamwa mwa wopusa mumuononga, milomo yake ikhala msampha wa moyo wake.
Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye; kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira.
Yemwe adalitsa mnzake ndi mau aakulu pouka mamawa, anthu adzachiyesa chimenecho temberero.
Mau a m'kamwa mwa munthu wanzeru nga chisomo; koma milomo ya chitsiru idzachimeza. Chiyambi cha mau a m'kamwa mwake ndi utsiru; ndipo chimaliziro cha m'kamwa mwake ndi misala yoipa.
Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efuremu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m'chigwa cha nthaka yabwino. Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono. Iai, koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa; amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva. Chifukwa chake mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa. Chifukwa chake imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a mu Yerusalemu. Chifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tavomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga; chifukwa chake Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika mu Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangodya, wa mtengo wake wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira. Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chilili; ndipo matalala adzachotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo. Ndipo pangano lanu ndi imfa lidzathedwa, ndi kuvomerezana kwanu ndi kunsi kwa manda kudzalephereka; popita mliri woopsa udzakuponderezani pansi. Nthawi zonse umapita, udzakutengani; chifukwa m'mawa ndi m'mawa udzapita, usana ndi usiku; ndipo kudzakhala kuopsa kokha, kumva mbiri yake. Taonani, Ambuye ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.
Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda.
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
Kotero lilimenso lili chiwalo chaching'ono, ndipo lidzikuzira zazikulu. Taonani, kamoto kakang'ono kayatsa nkhuni zambiri! Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.
Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira.
Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.
Mau onsetu onenedwa usawalabadire; kuti usamve kapolo wako alikukutemberera; pakuti kawirikawiritu mtima wako udziwa kuti nawenso unatemberera ena.
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza. Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.
Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.
Chifukwa chake Mulungu anawapereka iwo m'zilakolako za mitima yao, kuzonyansa, kuchititsana matupi ao wina ndi mnzake zamanyazi; amenewo anasandutsa choonadi cha Mulungu chabodza napembedza, natumikira cholengedwa, ndi kusiya Wolengayo, ndiye wolemekezeka nthawi yosatha. Amen.
Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima; pakuti tili ziwalo za thupi lake. Chifukwa cha ichi munthu azisiya atate ndi amai, nadzaphatikizana ndi mkazi wake; ndipo iwo awiri adzakhala thupi limodzi. Chinsinsi ichi nchachikulu; koma ndinena ine za Khristu ndi Mpingo. Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna. kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:
iyeyo watukumuka, wosadziwa kanthu, koma ayalukira pa mafunso ndi makani a mau, kumene zichokerako njiru, ndeu, zamwano, mayerekezo oipa;
Koma apatsa chisomo choposa. Potero anena malembo, Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo odzichepetsa.
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?
Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara! Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere. Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.
Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka. Monga makala ozizira pa makala akunyeka, ndi nkhuni pamoto; momwemo munthu wamakangano autsa ndeu. Mau a kazitape ndi zakudya zolongosoka zitsikira m'kati mwa mimba.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Mverani Ine, inu amene mudziwa chilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope chitonzo cha anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
koma ndinena kwa inu, Musakanize munthu woipa; koma amene adzakupanda iwe pa tsaya lako lamanja, umtembenuzire linanso.
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru. Pakuti nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, Iye agwira anzeru m'chenjerero lao;
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro. Taonani, malembedwe aakuluwo ndakulemberani inu ndi dzanja langa la ine mwini. Onse amene afuna kuonekera okoma m'thupi, iwowa akukakamizani inu mudulidwe; chokhacho, chakuti angazunzike chifukwa cha mtanda wa Khristu. Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu. Koma kudzitamandira ine konsekonse, iai, koma mu mtanda wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene mwa Iye dziko lapansi lapachikidwira ine, ndi ine ndapachikidwira dziko lapansi. Pakuti mdulidwe ulibe kanthu, kusadulidwa kulibe kanthunso, komatu wolengedwa watsopano. Ndipo onse amene atsata chilangizo ichi, mtendere ndi chifundo zikhale pa iwo, ndi pa Israele wa Mulungu. Kuyambira tsopano palibe munthu andivute, pakuti ndili nayo ine m'thupi mwanga mikwingwirima ya Yesu. Chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu chikhale ndi mzimu wanu, abale. Amen. Nyamuliranani zothodwetsa, ndipo kotero mufitse chilamulo cha Khristu.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
Alipo golide ndi ngale zambiri; koma milomo yodziwa ndiyo chokometsera cha mtengo wapatali.