Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 26:24 - Buku Lopatulika

24 Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau aakulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Koma pakudzikanira momwemo, Fesito anati ndi mau akulu, Uli wamisala Paulo; kuwerengetsa kwako kwakuchititsa misala.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Pamene Paulo ankadziteteza ku zomnenezazo, Fesito adanena mokweza mau kuti, “Misalatu imeneyi, iwe Paulo! Kuphunziritsa kwako kukukupengetsa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Paulo akudziteteza, Festo anakweza mawu nati, “Wazungulira mutu Paulo! Kuphunzira kwako kwakuchititsa misala.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 26:24
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehu anatulukira kwa anyamata a mbuye wake, nanena naye wina, Mtendere kodi? Anakudzera chifukwa ninji wamisala uyu? Nanena nao, Mumdziwa munthuyo ndi makambidwe ake.


Yehova anakuyesa iwe wansembe m'malo mwa Yehoyada wansembe, kuti iwe ndi anzako mudzakhale akapitao m'nyumba ya Yehova, oyang'anira munthu yense wamisala, wodziyesa mneneri, kuti umuike iye m'zigologolo ndi m'goli.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Ndipo pamene abale ake anamva, anadza kudzamgwira Iye; pakuti anati adayaluka.


Chifukwa chake Ayuda anazizwa, nanena, Ameneyu adziwa bwanji zolemba, wosaphunzira?


Ayuda anayankha nati kwa Iye, Kodi sitinenetsa kuti Inu ndinu Msamariya, ndipo muli ndi chiwanda?


Ayuda anati kwa Iye, Tsopano tazindikira kuti muli ndi chiwanda. Abrahamu anamwalira, ndi aneneri; ndipo Inu munena, Munthu akasunga mau anga, sadzalawa imfa kunthawi yonse.


Ndipo pamene anamva za kuuka kwa akufa ena anaseka pwepwete; koma ena anati, Tidzakumvanso za chimenechi.


Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.


Ndipo m'mene anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruziro chilinkudza, Felikisi anagwidwa ndi mantha, nayankha, Pita tsopano; ndipo ndikaona nthawi, ndidzakuitana iwe.


Koma zitapita zaka ziwiri Porkio Fesito analowa m'malo a Felikisi; ndipo Felikisi pofuna kukonda Ayuda anamsiya Paulo m'nsinga.


Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.


koma ife tilalikira Khristu wopachikidwa, kwa Ayudatu chokhumudwitsa, ndi kwa amitundu chinthu chopusa;


Tili opusa ife chifukwa cha Khristu, koma muli ochenjera inu mwa Khristu; tili ife ofooka, koma inu amphamvu; inu ndinu olemekezeka, koma ife ndife onyozeka.


Pakuti ngati tili oyaluka, titero kwa Mulungu; ngati tili a nzeru zathu, titero kwa inu.


ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa