Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo pamene anatha kumchitira Iye chipongwe, anavula malaya aja, namveka Iye malaya ake, natsogoza Iye kukampachika pamtanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Ataseŵera naye mwachipongwe choncho, adamuvula chovala chija namuvekanso zovala zake. Kenaka adamtenga, nkupita naye kuti akampachike pa mtanda.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Atamaliza kumuchitira chipongwe, anamuvula malaya aja namuveka malaya ake aja napita naye kokamupachika.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:31
12 Mawu Ofanana  

ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.


Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mzinda, namponya miyala, namupha.


Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Amuphe munthuyu ndithu; khamu lonse limponye miyala kunja kwa chigono.


nadzampereka kwa anthu akunja kuti amnyoze ndi kumkwapula, ndi kumpachika; ndipo Iye adzaukitsidwa tsiku lachitatu.


Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.


Mudziwa kuti akapita masiku awiri, Paska afika, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kupachikidwa pamtanda.


Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.


Ndipo pamenepo anampereka Iye kwa iwo kuti ampachike. Pamenepo anatenga Yesu;


Pamene ananena kwa wophunzirayo, Taona, amai wako. Ndipo kuyambira ora lomweli wophunzirayo ananka naye kwao.


ndipo anamtaya kunja kwa mzinda, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.


Mwa ichi Yesunso, kuti akayeretse anthuwo mwa mwazi wa Iye yekha, adamva chowawa kunja kwa chipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa