Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:30 - Buku Lopatulika

30 Namthira malovu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 Namthira malovu, natenga bango, nampanda Iye pamutu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 Adamthira malovu, natenga ndodo ija nkumamumenya nayo m'mutu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 Anamuthira malovu ndipo anatenga ndodo namumenya nayo pa mutu mobwerezabwereza.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:30
12 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Mombolo wa Israele, ndi Woyera wake, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyasidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira chifukwa cha Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israele, amene anakusankha Iwe.


Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisire nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.


Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu;


Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi wodziwa zowawa; ndipo ananyozedwa monga munthu wombisira anthu nkhope zao; ndipo ife sitinamlemekeze.


Iye anatsenderezedwa koma anadzichepetsa yekha osatsegula pakamwa pake; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwanawankhosa amene ali duu pamaso pa omsenga, motero sanatsegule pakamwa pake.


Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.


Pomwepo iwo anathira malovu pankhope pake, nambwanyula Iye; ndipo ena anampanda khofu,


ndipo adzamnyoza Iye, nadzamthira malovu, nadzamkwapula Iye, nadzamupha; ndipo pofika masiku atatu adzauka.


Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.


Ndipo anampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malovu, nampindira maondo, namlambira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa