Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:41 - Buku Lopatulika

41 Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

41 Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani; kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu, ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

41 “ ‘Mvetsani inu anthu onyoza, zizwani ndipo muwonongeke, pakuti pa nthaŵi ya moyo wanu Ine ndidzachita chinthu chimene simungakhulupirire konse, ngakhale wina akuuzeni.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

41 “ ‘Onani, inu anthu onyoza, dabwani ndipo wonongekani, chifukwa ine ndidzachita china chake mʼmasiku anu, inu simudzazikhulupirira ngakhale wina atakufotokozerani!’ ”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:41
26 Mawu Ofanana  

ndi kuti, Bwanji ndinada mwambo, mtima wanga ndi kunyoza chidzudzulo;


Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.


Ndipo mudzasiya dzina lanu likhale chitemberero kwa osankhidwa anga, ndipo Ambuye Yehova adzakupha iwe, nadzatcha atumiki ake dzina lina;


Koma ukachenjeza woipa za njira yake, aileke; koma iye osaileka njira yake, adzafa m'mphulupulu mwake iye, koma iwe walanditsa moyo wako.


Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.


Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka.


Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.


Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti, Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu, kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.


Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwa amitundu.


Ndipo kudzali, kuti wamoyo aliyense samvera mneneri ameneyu, adzasakazidwa konse mwa anthu.


pakuti tinamumva iye alikunena, kuti, Yesu Mnazarayo amene adzaononga malo ano, nadzasanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.


natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza machimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira chimaliziro.


Chifukwa yafika nthawi kuti chiweruziro chiyambe pa nyumba ya Mulungu; koma ngati chiyamba ndi ife, chitsiriziro cha iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu chidzakhala chiyani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa