Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:40 - Buku Lopatulika

40 Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Ndiye inu chenjerani kuti zingakugwereni zimene aneneri aja adanena kuti,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Samalani kuti zimene aneneri akunena zisakuchitikireni inu:

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:40
13 Mawu Ofanana  

chifukwa chake, taonani, ndidzachitanso mwa anthu awa ntchito yodabwitsa, ngakhale ntchito yodabwitsa ndi yozizwitsa; ndipo nzeru ya anthu ao anzeru idzatha, ndi luntha la anthu ao ozindikira lidzabisika.


Koma ukachenjeza woipa za njira yake, aileke; koma iye osaileka njira yake, adzafa m'mphulupulu mwake iye, koma iwe walanditsa moyo wako.


Penyani mwa amitundu, penyetsetsani, nimudabwe kwakukulu, pakuti ndichita ntchito masiku anu, imene simudzavomera chinkana akufotokozerani.


Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;


Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng'anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa. Adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.


Ndipo anati kwa iwo, Awa ndi mauwo ndinalankhula nanu, paja ndinakhala ndi inu, kuti ziyenera kukwanitsidwa zonse zolembedwa za Ine m'chilamulo cha Mose, ndi aneneri, ndi Masalimo.


Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi Mulungu. Yense amene adamva kwa Atate, naphunzira, adza kwa Ine.


Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa,


Koma Mulungu anatembenuka, nawapereka iwo atumikire gulu la kumwamba; monga kwalembedwa m'buku la aneneri, Kodi mwapereka kwa Ine nyama zophedwa ndi nsembe zaka makumi anai m'chipululu, nyumba ya Israele inu?


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa